Nkhani

Ulendo wa chisankho wapsa

Listen to this article

Zipani zina zati bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) liyenera kukwaniritsa zomwe lidalonjeza sabata yatha kuti chisankho cha 2019 chidzayenda mosakondera mbali.

MEC idakhazikitsa ulendo wa chisankho chimene chidzakahalepo pa 21 May 2019 ndi lonjezo limodzi: Palibe kukondera.

Wachiwiri kwa mlembi wamkulu wa chipani cha Malawi Congress (MCP) Eisenhower Mkaka adati lonjezo lotereli limanenedwa nthawi zonse kumayambiriro kwa ulendo ngati kuno koma pamapeto pake zimaoneka ndi zina.

“Tili ndi chikhulupiliro kuti ulendo uno, MEC isunga lonjezo lake ndipo tiziyang’anira kuti lonjezoli akulikwaniritsa motani? Vuto ndiloti timamva lonjezo lomwelomwelo nthawi zonse koma kumapeto timaona zina,” adatero Mkaka.

Mneneri wa chipani cha Peoples’ Party (PP) Noah Chimpeni wati nkhawa yawo ili pakusasunga lonjezo kwa bungwe la MEC lomwe nthawi zambiri limawoneka kuti limapereka mpata waukulu ku mbali ina.

“Nthawi zonse amatero koma sitidaonepo umboni oti akwaniritsa lonjezoli. Ngati akunena za chilungamo, ndiye awonetsetse kuti chipani chilichonse chizikhala ndi mpata ofanana ngakhale pa MBC osati olamula okha ayi,” adatero Chimpeni.

Iye adati pakhalenso ndondomeko yoonetsetsa kuti aliyense azikhala ndi mpata wa msonkhano kulikonse komwe wafuna chifukwa nthawi zina misonkhano ina amayiletsa nthawi yothaitha ponena kuti kumaloko kukupita mtsogoleri wa dziko.

Chipani cha United Democratic Front (UDF) chati aka sikoyamba chipanichi kumva lonjezo lotere kuchokera ku bungwe la MEC koma chomwe chimavuta n’kukwatitsa lonjezoli ndi zochitika.

Mneneri wachipani cha UDF Ken Ndanga adati chipani chawo chimafuna ntchito zooneka ndi maso osati mawu chabe.

“Sikoyamba kumva mawu amenewa kuchoka pakamwa pa MEC. Zakhala zikunenedwa koma chimavuta n’kukwaniritsa mawuwo. Nkhani yaikulu ndi ntchito osati mawu chifukwa anthu timakhala tikuona zochitika,” adatero Ndanga.

Mlembi wamkulu wa chipani cha Alliance For Democracy (Aford) Christopher Ritchie wati chipani chawo chitsatira ndondomeko zomwe MEC yakhazikitsa koma nacho chiyembekezera MEC kukwaniritsa mbali yake monga mwa lonjezo.

“Paliponse pamafunika chilungamo kuti zinthu ziyende bwino ndipo ife a Aford timakhulupilira chilungamo. Choncho, titsatira ndondomeko koma nawonso akwaniritse zomwe alonjeza osati tidzawone zina kumapeto,” adatero Ritchie.

MEC idatsegulira ulendowu pa 20 February 2018 ndipo zipani za ndale zati kupatula zokonzekera zina ndi zina, maso awo ali pa lonjezo lomwe bungweli lidapereka kuti chisankhocho chidzakhala chopanda zitopotopo.

Wapampando wa MEC Jane Ansah adalonjeza kuti chisankho cha 2019 chidzakhala chokomera aliyense chifukwa bungwelo lilibe mbali iliyonse yoti mwina ena azikayika kuti pangadzakhale kukondera.

“Bungwe la MEC ndilodzipereka kuchititsa chisankho cha mtendere ndi chokomera aliyense. Paulendo onse mpaka kumapeto, pakhala chilungamo ndi kuika zinthu pamtetete ndipo sitidzasekerera ogwira ntchito ku MEC aliyense opanga zautambwali,” adatero Ansah.

Iye adati bungwelo likuyembekezeranso mgwirizano kwa onse okhudzidwa ndi chisankho chomwe chikudzachi ndipo kuti zikatero, nalo (bungwe la MEC) lidzayesetsa kuti lisaopsezedwe kapena kutumidwa ndi mbali kapena mphamvu iliyonse.

Ansah adati makomo a MEC akhala otsegula paulendo onse ndipo bungwelo lidzalandira ndi kuchitapo kanthu pa dandaulo lililonse lomwe okhudzidwa angadzabweretse mosaona nkhope.

Koma zipani zina za ndale zati zamva lonjezoli koma maso ake akhala akuyang’anitsitsa pa MEC kuti zione komwe lonjezoli lizilowera mpaka komwe likathere.

Bungwe loona za kayendetsedwe ka ndale za zipani zambiri la Centre for Multiparty Democracy (CMD) lati paulendowu mpofunika kugwirana manja pakati pa mbali zosiyanasiyana kuti tikafike bwino.

Wapampando wa bungwelo Kandi Padambo adati magulu monga zipani za ndale, nyumba zofalitsa nkhani ndi boma makamaka oyang’anira thumba la chuma akuyenera kutengapo mbali kwambiri.

“Ku mbali ya boma, mpofunika kupereka ndalama zoyendetsera chisankho zokwanira nthawi yabwino,” adatero Padambo.

Related Articles

Back to top button