UTM Ilembetsa ngatichipani—Malunga

Ulendo wapsa. Ali ndi mwana agwiritse. Eni basiyo akuti siiphwa matayala mpaka ikafika ku zisankho zapatatu za chaka cha mawa.

Iyi ndi basi ya United Transformation Movement (UTM) yomwe dalayivala wake ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Saulos Chilima.

Akuti adzathetsa ziphuphu: Chilima

Mneneri wa gululi Joseph Chidanti Malunga adati UTM si chipani cha ndale, koma posachedwapa lilembetsa ngati chipani “pofuna kuchotsa chikayiko m’mitima ya anthu kuti chikapitiriza kugwira ntchito zake ngati gulu mwina chikhoza kukumana ndi zokhoma zina.

“Malamulo a dziko lino tikuwadziwa ndipo tikudziwa zotsatira zosalembetsa m’kaundulu wa zipani za ndale.

“Amalawi asade nkhawa chifukwa nkhaniyi tikuyiunika ndipo zotsatira zake tilengeza posachedwapa.”

Potengera ndi malamulo azisankho, UTM ikuyenera kulembetsa ngati chipani cha ndale, osati gulu chabe, kuti masomphenya ake osatchonera panjira akwaniritsidwe.

Kadaulo pa ndale wa ku sukulu yaukachenjede ya Chancellor College, Henry Chingaipe, adati UTM ikuoneka ngati siidabwere mocheza, ikudziwa zomwe ikuchita ndipo zipani zina zichenjere.

Chingaipe adati ali ndichikhulupiliro choti gululi likwanitsa masomphenya ake wodzaimitsa pulezidenti ndi aphungu pa zisankho za chaka cha mawa.

“UTM yachenjera popanga mgwirizano ndi chipani cha United Transformation Party (UTP) potengera ndi mikwingwirima yomwe zipani zimakumana nayo pofuna kulembetsa,” adatero katswiriyu.

Chingaipe adati gululi litha kudzangodziwitsa ofesi yakalembera wa zipani kuti magulu awiriwa asanduka gulu limodzi.

Malunga watsimikuza zoti UTM ndi UTP si magulu awiri, koma limodzi.

Gulu la UTM, lomwe lidakhazikitsidwa Loweruka lapitali, lati lidzaimitsa pulezidenti, komanso aphungu m’madera onse 193 omwe amaimiliridwa ku Nyumba ya Malamulo.

Malamulo azisankho amati “munthu akhoza kupikisana nawo pa upulezidenti, uphungu kapena ukhansala poima payekha kapena kuimira chipani cha ndale chodziwika ndi ofesi yakalembera wazipani”.

Pomasulira lamuloli mogwirizana ndi kubwera kwa UTM, Chingaipe adati gululi likhoza kudzapita kuchisankho ngakhale osasintha dzina bola kulowa m’kaundula wa zipani za ndale.

“Dzina lilibe ntchito. Pali zipani zambiri zomwe maina awo sasonyezeratu kuti ndi zipani za ndale. Koma chifukwa zidalembetsa, zimapikisana nawo pa zisankho. N’chimodzimodzi UTM,” adatero katswiriyu.

Malunga adati UTM ili pakalikiliki kukhazikitsa maziko m’maboma onse a m’dziko muno moti posachedwapa ntchitoyo ikhala itatha.

UTM yakhazikitsa ndondomeko 10 zotukulira dziko lino ndipo zina mwa izo ndi kuthana ndi mchitidwe wa katangale, kuonetsetsa kuti Amalawi ndi wotetezedwa kuphatikizirapo maalubino, kuthana ndi kuzimazima kwa magetsi, kuchepetsa umphawi, kuthana ndi kusalana mitundu ndi zina.

Share This Post