Wakuba ufa ndi makala agamulidwa zaka 4
Bambo Cosmas Chiwambo, a zaka 22, omwe amachokera m’mudzi mwa Mwamadi kwa T/A Chikumbu m’boma la Mulanje, alamulidwa kuti akakhale ku ndende kwa zaka zinayi atapezeka wolakwa pa mlandu wothyola nyumba ndi kubamo ufa komanso thumba la makala.
Bwalo la Senior Resident ku Mulanje lidamva mlanduwo motsogozedwa ndi woimira boma pa milandu, a constable Paul Nsindo, kuti pa 20 May, 2025, a Andrew Messia, omwe ndi wodandaula, adalandira uthenga kuchokera kwa mlonda wawo kuti iwo adaona bamboo Cosmas Chiwambo, akulowa m’nyumba mwa bambo Messia pakati pa usiku koma mwatsoka, adathawa atazindikira kuti mlondayo adamuona.

Ndipo m’mawa wa tsikulo, wodandaulayo adadzidzimuka ataona kuti ufa wa chimanga wolemera makilogalamu 5 komanso thumba la makala, zidasowa m’nyumbamo.
Choncho iwo adatengera nkhaniyo ku polisi ya Mathambi, omwe apolisi adachita kafukufuku wawo ndipo pakutha pa ntchitoyo, a Chiwambo adamangidwa.
A Nsindo adati apolisiwo adamukwizinga ndi mafunso omwe pamapeto pake adampeza ndi mlandu wothyola nyumba ndi kuba katundu, zomwe wakubayo adavomera mwa changu.
Nthawi yomwe adakaonekera ku bwalo la milandu, iwo sadachedwetse a khoti koma kuvomereza tchimo lawo koma adapempha bwalolo kuti liwamvere chisoni chifukwa kudali oyamba kuba.
Koma woimira boma pa milandu, a Nsindo adatsindika za kufunika kopereka chilango chokhwima chifukwa choti adawopseza chitetezo cha m’mudzi, zomwe adanenetsa kuti anthu adayamba kukhala mwa mantha kuopa atsinzinamtolewo.
Popereka chigamulo, woweruza milandu pa khotilo, a Gloria Mwatiwamba, adavomerezana ndi a mbali ya boma kuti Chiwambo amayenera kulandira chilango chokhwima kuti likhalenso phunziro kwa ena ochita za upanduzo.
Motero, a Mwatiwamba, adagamula bambo Chiwambo kuti akakhale zaka zinayi pa mlandu wothyola ndiponso miyezi 6, pa mlandu woba ufa ndi makala, yomwe iyendere limodzi.



