Wodzaima pa mpando wa pulezidenti azapereka K2m

Bungwe la Malawi Electoral Support Network (Mesn) ladzudzula bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) pokweza ndalama zomwe anthu ofuna kudzaima nawo pa zisankho zapatatu za chaka cha mawa azipereka.

Mkulu wa bungwe la MEC, Jane Ansah, Lachiwiri mu mzinda wa Lilongwe adalengeza kuti aliyense yemwe akufuna kudzaima nawo pa zisankho za mtsogoleri wa dziko lino akuyenera kudzapereka K2 miliyoni pamene abambo omwe adzapikitsane nawo pa mipando ya aphungu a Nyumba ya Malamulo adzapereka K500 000 ndipo amayi adzapereka K250 000.

Adzaimira MCP: Chakwera

 

Ansah adalengezanso kuti abambo omwe akufuna kudzapikitsana nawo ngati makhansala akuyenera kudzapereka K40 000 pamene amayi adzapereka K20 000.

Koma mkulu wa bungwe la Mesn, Steve Duwa, wauza Tamvani kuti kusinthaku kubwezera mmbuyo anthu ena omwe akufuna kudzapikitsana nawo pa zisankhozo, koma m’thumba mwawo ndi moperewera.

Duwa wati ndiwokhumudwa kuti sipadathe nthawi yayitali MEC chikwezereni ndalamazo.

MEC idakwezanso ndalamazo pa zisankho zapatatu za mu 2014 ndipo mabungwe osiyanasiyana omwe akulimbikitsa amayi kutenga nawo gawo pa ndale za dziko lino adadandaulanso kuti kusinthako kubwezera mmbuyo kampeni yawo.

“MEC yapupuluma imayenera kudikira kuti papite zisankho zingapo isadakwezenso osati kumangokweza pa chisankho chilichonse chifukwa uku n’kupweteka anthu omwe sangakwanitsa kupeza ndalama,” adatero Duwa.

Adzaimira DPP: Mutharika

Ngakhale malamulo oyendetsera zisankho amapereka mphamvu kwa bungwe la MEC kukweza ndalama zomwe anthu amapereka, koma Duwa adati mphamvuzo n’zofunika kuzigwiritsa ntchito moyenera pokambirana ndi zipani za ndale kukwezako kusadachitike.

Koma Ansah adati akuluakulu a bungwelo adakambirana ndipo adaona kuti kukwezako n’koyenera.

Mkuluyu adati ndondomeko zina zonse zoyendetsera zisankho sizidasinthe.

Ansah adapempha zipani zandale kuti zitsatire ndondomeko zonse kaamba koti munthu akadzapezeka kuti ndiwosayenera adzamuthothola ndipo sipadzakhala mwayi woti chipani chake chidzapereke dzina la  munthu wina.

Ansah adakumbutsanso zipani ndi onse omwe akufuna kudzaima nawo pa zisankho za chaka cha mawa kuti aliyense amene amagwira ntchito m’boma ndipo akufuna kudzapikisana nawo pa zisankhozo akuyenera kutula kaye pansi udindo wake asadabwere poyera.

Padakali pano zipani zina za ndale zomwe zidaonetsa chidwi chofuna kudzapikisana nawo pa zisankhozo zidapangitsa kale misonkhano yawo yosankha atsogoleri moti panopa zikupangitsa mapulayimale wosankha anthu omwe adzaziimire pa mipando ya aphungu ndi makhansala.

Chipani cha Malawi Congress (MCP) chidasankha mtsogoleri wake Lazarus Chakwera kuti ndiye adzachiimire pa zisankho za chaka cha mawa pamene mtsogoleri wa Democratic Progressive (DPP) Peter Mutharika adzaimira chipanicho.

Share This Post