Zionetsero zaima

Anthu zikwizikwi adabwerera manja ali m’khosi kuchoka m’malo a zionetsero Lachitatu pa 28 August 2019 atauzidwa kuti zionetserozo

zalephereka kaamba ka chiletso cha khoti la Supreme mumzinda wa Blantyre.

Chitetezo chidali chokhwima

Izi ndi zionetsero zomwe a Human Rights Defenders Coalition (HRDC) adakonza kukachitira m’mabwalo a ndege komanso m’zipata zonse za dziko lino kwa masiku atatu kuyambira Lachitatu mpaka dzulo Lachisanu.

“Titaunika mfundo za opempha chiletso, chigamulo n’choti kwa masiku 14 kuyambira Lachitatu pa 28 August, 2019 kusachitike chionetsero cha mtundu uliwonse, panthawiyi, mbali ziwiri ya boma ndi HRDC zikumane n’kukambirana momwe anthu angadyerere ufulu wawo wopanga zionetsero komanso pasapezeke munthu wolankhula zomwe zingasokoneze mlandu wa chisankho,” chikutero chiletsocho.

Koma pakucha Lachitatu, kudaonetsa kuti ena adasemphana ndi

uthengawo chifukwa anthu adayamba kukhamukira mmalo omwe HRDC idalengeza kuti mudzayambira zionetserozo.

Mmawa momwe, apolisi komanso asilikali adali mbwee m’mizinda kufuna kuonetsetsa kuti anthu atsatira chigamulo cha khoti la Supreme koma izi sizidakomere anthu ena omwe adakonzekera kuonetsa mkwiyo wawo.

“Kodi anthu amenewa bwanji? Chikuwaopsa n’chiyani? Bwanji

akunjenjemera okhaokha? Akadatisiya tipange zionetsero bwinobwino mesa ndi ufulu wathu? Bomalitu likutiponderedza kwambiri,” adatero Mathews Kawinga yemwe amakhala ku Mtandire mumzinda wa Lilongwe.

Pulogalamu ya zionetserozi idagwedeza dziko moti Lachitatu mabizinesi ambiri komanso maofesi ena adali otseka poopa zomwe zakhala zikuchitika pazionetsero zina pomwe anthu ena amatengerapo mwayi n’kumathyola maofesi komanso sitolo za anthu n’kumaba.

Zionetsero zomwe zikuchitika m’dziko muno n’zofuna kuchotsa wapampando wa Malawi Electoral Commission (MEC) Jane Ansah chifukwa Amalawi ena akuti sadayendetse bwino chisankho chathachi.

Koma HRDC yatsimikizira Amalawi kuti akatha masiku 14 omwe khothi lapereka, zionetserozo zidzapitilira mopanda mantha aliwonse ngakhale akuopsezedwa.

Mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika adalamula apolisi ndi asilikali ankhondo kuti adzagwiritse ntchito mphamvu, zida ndi njira iliyonse kuti zionetsero zisadzachitike.

Mutharika adalankhula izi pamwambo wotsegulira sitima za nkhondo ku Mangochi pa 20 August 2019 koma akadaulo pa ndale ndi malamulo adati Mutharika adalakwitsa chifukwa kuteroko nkuponderedza ufulu wa anthu omwe uli mmalamulo omwe iye adalumbira kuti adzalemekeza.

Share This Post