Nkhani

Zipani zikufuna mayankho pa zitupa za unzika

Listen to this article

Zipani za Malawi Congress Party (MCP) ndi People’s Party (PP) zati kusowa kwa zitupa zina za olembetsa m’kaundula wa unzika zidzasokoneza chisankho cha patatu cha 2019.

Nthambi ya National Registration Bureau (NRB) yati mwa zitupa 1.7 miliyoni zomwe zidajambulidwa m’gawo loyamba la zitupa za unzika, 1.5 miliyoni ndizo zatuluka. Izi zili choncho, bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lati lidzagwiritsabe ntchito zitupazo polembera ovota.

Mlembi wa PP Ibrahim Matola adati zitupazo sizimayenera kugwiritsidwa ntchito m’kalembera wa ovota chifukwa ntchitoyi siyinakhazikike.

“Tangoyamba kumene ntchitoyi. Tisayidalire ayi bola mtsogolomu zikadzagwira msewu koma padakalipano tiyeni tigwiritse ntchito njira yomwe timagwiritsa nkale lonse,” adatero Matola.

Mneneri wa chipani cha MCP Eisenhower Mkaka adati zitupa za unzika zokha sizikuyenera kugwiritsidwa ntchito pa mavoti chifukwa zina zikusowa.

“Kudzazigwiritsa ntchito limodzi ndi zitupa zovotera osati pazokha ayi poopa libolonje,” adatero iye.

Phungu wa ku mmawa kwa boma la Dowa, Richard Chimwendo-Banda wa MCP, adati kufaifa kwa zipangizozo kukhoza kuchititsa kuti anthu ambiri m’chigawo cha pakati asadzakhale ndi zitupa ndikulephera kudzaponya nawo voti.

Mkaka: Alongosole

Mneneri wa MEC Sangwani Mwafulirwa watsindika kuti zitupazo zidzagwiritsidwa ntchito popanga kaundula wa odzavota pa chisankho cha 2019.

“Munthu amene adzakhale ndi chitupa, n’zachidziwikire kuti ndi nzika ndiye sitidzalimbana naye zambiri komabe tidzaona momwe tidzathandizire omwe alibe zitupa,” adatero Mwafulirwa.

Iye adati MEC ikuyembekezeka kudzayamba kukonza kaundula wa odzavota ndipo akukhulupilira kuti pofika nthawi yamavoti, nzika iliyonse idzakhala italandira chitupa chake.

Mneneri wa nthambi ya NRB Norman Fulatira wati anthu asakhale ndi nkhawa pankhaniyo chifukwa zivute zitani, Amalawi onse adzakhala ndi zitupazo.

Related Articles

Back to top button
Translate »