Nkhani

Zitukuko zothandiza Amalawi zisamafe

Listen to this article

Patha zaka 50 kuchokera pamene dziko lino lidalandira ufulu wodzilamulira. Tikaunikira bwino momwe chuma chikuyendera m’dziko muno poyerekeza ndi momwe zili m’maiko ena amene tidalandira nawo ufulu limodzi, zimakhala zomvetsa chisoni kuti tili kumbuyo zedi.

Dziko lino lakhala lili ndi atsogoleri atatu ndipo aliyense amabwera ndi nzeru zake za momwe angatukulire dziko lino. Koma zimakhala zomvetsa chisoni kuti ntchito zina zabwino zimaimitsidwa mtsogoleri akachoka kubwera wina.

Izi zimakhala choncho makamaka chifukwa amene walowa pampando amafuna kuonetsa kuti amene adalipo iye asadalowe pampando adalephera kutukula dziko lino.

Tigwirizane ndi amene akunena kuti izi zikuchititsa kuti chuma cha boma chisakazike, chifukwa pofika poimika chitukukocho, ndalama zimakhala zitalowapo kale.

Vuto lalikulu likumakhalanso chifukwa chakuti nthawi zambiri atsogoleri amangoyamba ntchitozi mwa okha, osachita kudutsa ku Nyumba ya Malamulo, zimene zimasonyeza kuti ntchitozo ndi maloto awo chabe.

N’chifukwa chake tikuti, ntchito za chitukuko zosalingalira Amalawi zili chabe. Ntchito zongofuna kuti atsogoleri aoneke ngati ndi achitukuko koma zili zopanda tsogolo lenileni zilibe phindu.

Related Articles

Back to top button