Nkhani

Kusamala ndi antchito olera ana

Ana ambiri masiku ano akuleredwa ndi antchito m’makomomu popeza makolo awo amakhala otangwanika kusaka makobidi kuntchito kapena mabizinezi.

Ndipo alipo ena antchito odziwa kulera mwana mwachikondi oona n’kumadabwa kuti zoterezi zikutheka bwanji, koma si onse antchito omwe amaika mtima posamala mwana wa bwana. Ena ngankhanza; ena achibwana; ena amgwazo ndipo kupanda kupenyetsetsa bwino akhonza kubweretsa mavuto pamoyo wa ana komanso banja.

Nthawi zina chifukwa cha kutangwanika makolo amalephera kuonetsetsa kuti ana awo akuleredwa bwanji pakhomo. Makolo ena amangotayirira chilichonse nkusiya m’manja mwa anthu omwe kwawo kumakhala kungothandizira kaleredwe ka ana.

Antchito enanso chidwi chawo sichikhala kwenikweni posamalira mwana, koma pa ndalama zomwe amalandira mwezi ukatha.

Poterepa pamafunika kupenyetsetsa.

Tamvapo za antchito ena omwe mwana akawavuta ndi kulira amatha kungomuyamwitsa, mmalo momupatsa mkaka wam’botolo.

M’makomo momwe miswachi imangounjikidwa kubafa, antchito ena wawo mswachi ukatalikira amangotolapo wa mwana n’kutsukira mkamwa mwawo.

Kaya ndi chibwana kaya ndi umbuli, masiku ano a matenda opatsirana ngati Edzi, n’kwapafupi kuti mchitidwe ngati uwu ukhale chiopsezo kumoyo wa ana.

Antchito ena aulesi amangomusiya mwana muthewera loonongeka n’kungomusintha kapena kumusambitsa kumadzulo make akayandikira kubwera chonsecho tsiku lonseli mwana wakhalira kupsa muthewera losalongosoka.

Ana ena oliralira akukhalira kutsinidwa kapena kumenyedwa kumene ndi anthu othandizirawa, enanso omwe amakhalira kumudyera zakudya mwana, makolo n’kumangodabwa kuti sikelo ya mwana sikulongosoka.

Zilipo zambiri zomwe anthuwa amatha kuchita ndi ana omwe pokhala achichepere sangawiringule chilichonse.

Ngakhale pakhomo pali wothandizira, kumachitako chidwi kuti zinthu akuyendetsa bwanji.

Nanga anawo akuwasamalira bwanji chifukwa tsiku lina n’kudzalirira kuutsi.

Related Articles

Back to top button