Nkhani

Ati boma lisabweze ndalama ku FDH

Listen to this article

Anthu ena otsata mmene zinthu zikuyendera m’dziko muno aopseza kuti akonza zionetsero ngati boma limvere zonena za banki ya FDH kuti libwezeko K1.1 biliyoni mwa ndalama K9.5 biliyoni zomwe adagulitsira banki ya Malawi Savings Bank (MSB).

Sabata yatha zidadziwika kuti banki ya FDH yalembera boma kuti libweze ndalamazi ponena kuti padali zingapo zomwe sadaunikire bwino panthawi yogulitsanayo.

CFTC has just approved the merger of MSB and FDH Financial Holdings

Koma boma lakana kale kuti silibweza ndalamazo, zomwenso zasangalatsa othirira ndemanga kuti ndalamazi zisaperekedwe.

Mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wa ogula la Consumers Association of Malawi (CAMA) John Kapito wati boma lichite zomwe likulankhula.

“Zimatere kuti lero akutiuza kuti sabweza ndalamazo pamene kuseri apanga kale, tazionapo zotere zikuchitika. Pogulitsa bankiyi ife timati sagulitsa atatitsimikizira kuti satero koma mapeto ake tidamva kuti agulitsa.

“Lero boma litha kutilimbitsa mtima kuti sabweza ndalamazo koma mawa mumva kuti abweza kale. Ife tikupempha kuti chonde boma lisatero,” adatero Kapito.

Iye adati boma liganizire kuti zinthu sizili bwino m’dziko muno kumbali ya chuma ndipo ndi kulakwa kuti ndalama zipite m’njira zotere.

“Panopa tili pantchito yopeza ma triliyoni a bajeti ya dziko lino. Ndiye ngati tingapereke ndalamazi anthu akhala pamavuto chifukwa iyi ndi misonkho yathu,” adaonjeza Kapito.

Mu July 2015, boma lidagulitsa MSB ngakhale Amalawi ambiri adachenjeza kuti lisagulitse bankiyi. Koma mathero ake, boma lidagulitsabe bankiyi pamtengo wa K9.5 biliyoni.

Winanso womenyera ufulu wachibadwidwe, Martha Kwataine, wati zomwe zikuchitikazi ndi kubera Amalawi ndipo boma lisayerekeze.

“Banki idagulitsidwa pamtengo wotsika ndi kale, lero akuti tibwezenso ndalama zina, zoona? Ichitu n’chibwana ndipo Amalawi tisalole zimenezi. Ngati boma libweze ndalamazi kumbali ife osadziwa, ndiye timema Amalawi kuti tichite zionetsero chifukwa uku n’kutitengera pamgong’o,” adatero Kwataine.

Dr. Ephraim Chirwa, kadaulo pa zachuma kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, yomwe ndi nthambi imodzi ya Yunivesite ya Malawi, wati apa palibe nkhani chifukwa boma silidaswe pangano lililonse. n

Related Articles

Back to top button
Translate »