‘Mundibwezere voti yanga’, amalawi athafulira APM pazionetsero

Amalawi athera Chichewa mtsogoleri wa dziko lino komanso nduna zake pa zionetsero zomwe zidachitika Lachisau.

Zionetserozo zidatsogoleredwa ndi amipingo, amabungwe komanso azipani amene amakakamiza boma kuti liyankhepo pa mavuto amene dziko lino likudutsamo.

Mwa zina ndi kuuza mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika kuti athothe nduna ya zachuma Goodall Gondwe komanso ya maboma ang’ono Kondwani Nankhumwa pokhudzidwa ndi nkhani ya K4 biliyoni yomwe imagawidwa kwa aphungu 83 zisadasinthe kuti ziperekedwa kwa aphungu onse.

Amabungwewa akuda kukhosi ndi boma pankhani ya kuzimazima kwa magetsi chikhalirecho boma lidagula majeneleta kuti athane ndi kuzimazima kwa magetsiwo.

Patsikulo, mizinda ya Blantyre, Lilongwe, Zomba ndi Mzuzu komanso maboma monga Rumphi kudawirira pamene anthu adayenda kukapereka madandaulo awo kwa akuluakulu a boma.

Mwa zina, anthu adagwiritsa ntchito nyimbo popereka uthenga ku boma. Mwa nyimbo zina ndi monga: Tichotse nkhalamba ndi mtima umodzi. Bewu—bewula Peter, bewula Chaponda, bewula Goodall. Mukamva hi! Ho! agogo athawa, M’manja mwako mlamu tachokamo, undibwezere mavoti anga mlamu mwazina.

Ku Mzuzu, nyimbo idazunguza idali yolimbana ndi nduna zomwe zatopa ndi ukalamba m’boma.

“Mukutani m’boma, pitani muzikacheza ndi adzukulu kumudzi,” idatero.

Kupatula nyimbo, anthuwo adagwiritsiranso ntchito zikwangwani zomwe mudalembedwa mauthenga osiyanasiyana.

Mwa mauthengawo adali monga; Ngolongoliwa, Kyungu, Lukwa ndi Lundu si mafumu koma ogwira ntchito a chipani cha DPP.

Uthenga wina udalunga ku wailesi ya boma ya MBC. “Sumbuleta ndi Phillip Business, MBC si nyumba ya abambo anu.”

Uthenga wina umanena Gondwe: “Adada Goodall taweya mwachekula, lutani kukaya mukachezgenge nawazukulu [bambo Goodall mwakula, pitani kumudzi mudzikacheza ndi zidzukulu].”

Zina zimafunsa nkhani ya K4 biliyoni. “Kulubwalubwa ndi K4 biliyoni yathu?”

Mmodzi mwa akuluakulu amabungwe amene amatsogolera zionetserozi Gift Trapence wa bungwe la Centre for the Development of people (Cedep) adati zionetserozo zidachitika bwino.

“Ganizo lathu lakwaniritsidwa, tapereza madandaulo athu ku boma ndipo tikuwapatsa masiku 30 kuti atiyankhe ndipo akalephera kupitanso ku msewu,” adatero Trapence.  

Steven Pembamoyo, Martha Chirambo adathandizira pa nkhaniyi

Share This Post