NRB ionjezera masiku otengera zitupa

Ntchito yopereka zitupa za unzika kwa anthu a m’maboma 15 m’dziko muno, imene imayenera kutha dzulo ayionjezera m’boma la Blantyre, mneneri wa bungwe limene likuyendetsa ntchitoyi watero.

Maboma onse a chigawo chapakati komanso Blantyre, Mwanza, Neno, Nsanje ndi Chiradzulu ndiwo akulandira zitupazo m’gawo Lachiwiri ndipo malinga ndi mneneri wa bungwe la National Registration Bureau (NRB) Norman Fulatira adati bungwelo laonjezera sabata imodzi kuti anthuwo atenge zitupa zawo.

Fulatira Lachinayi adati: “Tionjezera sabata imodzi kuti anthu alandire ziphaso zawo ndipo ngati ena akhalebe asadatenge, zitupa zawo akatengera ziphaso zawo ku ofesi ya DC.”

Fulatira wati amene satenga zitupazo pakutha kwa kuonjezerako azikatengera zitupazo kuofesi ya DC wa boma lawo.

Kafukufuku wa Tamvani mumzinda wa Blantyre Lachinayi adavumbulutsa unyinji wa anthu akulimbirana kutenga zitupa ndipo anthu ena amene tidacheza nawo adati ndi bwino ntchitoyi ayionjezere.

Patrick Sandramu, yemwe adalembetsa kusukulu ya pulaimale ya Makata ku Ndirande mumzindawo, adati gulu likumakhala kotenga zitupako n’chiletso.

“Kufika lero Lachinayi, anthu ambiri sanatenge zitupa zawo ndipo gulu lake ndi losanena. Ine ndidachita mwayi chifukwa ndimadziwana ndi mmodzi mwa amene akugawa ziphaso ndipo ndidamuuza kuti akachipeza changa andisungire,” adatero mkuluyo.

Maxwell Majawa Lachinayi adati iye adati adayendera masiku angapo kusukulu ya Zingwangwa kuti atenge chitupa chake.

“Mbali imene amayendetsa aphunzitsi sizimavuta, koma kumene kumakhala anthu wamba ndiye mavuto analipo. Zoti tizipita kukatenga zitupa motsatira maina athu nazo zidatipomboneza. Ine ndidayendera masiku atatu kuti ndipeze chitupa,” adatero Majawa.

Ndipo Roselyne Manjawira amene adalembetsa kusukulu ya pulaimale ya Katete ku Chirimba adati pofika Lachinayi adali asanatenge chitupa chake chifukwa cha khamu, komanso chifukwa ameyenera kupita kuntchito.

“Akadaonjezera masiku chifukwa akanena kuti tizikatengera kwa a DC kukakhala chipwilikiti choopsa kuposa momwe zilili m’maderamu,” adatero iye.

Izi zili choncho, Madera ena, makamaka amene kulibe anthu ambiri, amatenga mosavuta.

Gawoli likatha, lisamukira m’boma la Thyolo, Chiradzulu ndi Mulanje.

Ndondomeko yopereka ziphasozi idayamba mu October chaka chatha ndipo ikuyembekezereka kutha mu March chaka chino.

Share This Post

One Comment - Write a Comment

Comments are closed.