Nkhani

Achenjeza zipani

Listen to this article

Akadaulo a zandale ena ati zomwe akuchita akuluakulu a zipani polekelera kukokanakokana m’zipani zawo n’kutsekeleza mwayi wodzapambana pachisankho cha 2019.

Katswiri wa za ndale kusukulu ya ukachenjede ya University of Livingstonia (Unilia) George Phiri komanso kadaulo pankhaniyi ku Chancellor College Happy Kayuni amathirira ndemanga pa kukokanakokana komwe kwayala nthenje m’zipani za Malawi Congress Party (MCP), Alliance for Democracy (Aford) ndi People’s Party (PP) pokanganirana utsogoleri ndi maudindo.

Mikwingwirima isanabuke: Msowoya ndi Chakwera

Koma azipanizo ati mkokemkokewu siukukolezera kulephera kwa zipanizo pachisankho chifukwa ayanjananso.

Phiri Lachiwiri adati atsogoleriwa azingotaya nthawi n’kulimbanaku uku nthawi ikupita mpaka adzanong’oneza bondo madzi ali m’khosi.

“Ino ndi nthawi yomanga ndi kumata ming’alu yonse yotsalira koma mmalo mwake, atsogoleri azipani akungokangana okhaokha. Pomwe azidzadzidzimuka, nthawi idzakhala itatha,” adatero iye.

Phiri adaonjeza kuti mikangano yotere, mapeto ake kumakhala kugawanika kwa akuluakulu komwe kumagawanso otsatira zipanizo mmalo mowamanga pamodzi kuti mavoti adzachuluke.

“M’chipani mumakhala akuluakulu osiyanasiyana omwe amakhala ndi owatsatira awo choncho, mgwirizano wa akuluakulu m’chipanimo, umabweretsanso mgwirizano pakati pa ochitsatira,” watero Phiri.

Iye adati zipani zambiri zomwe zili m’dziko muno chiyambi chake n’kugalukirana kwa atsogoleri posemphana pankhani ya mipando ndipo nthawi zambiri zimalowera ku malamulo a chipani.

Ndipo Kayuni adati mmalo momakangana, chipani cha nzeru nthawi ngati ino, chimakhala kalikiliki kuunika mphangala zoyenera kukopera anthu m’chipani.

Iye adagwirizana ndi Phiri kuti m’chipani chilichonse mumakhala akuluakulu omwe amakhala ndi anthu owatsatira kotero, chipani chimayenera kugwiritsitsa anthu oterowo kapena kukopa anthu otero kuti abwere mbali yawo.

“Chipani chanzeru nyengo ngati ino siyomakangana, chikuyenera kukhala pansi nkuona kuti ndi anthu ati omwe angabweretse mavoti kuchipani n’kukambirana ndi anthu oterowo kuti aphathane nawo,” watero Kayuni.

Nkhani yomwe ili mkamwamkamwa pano ndi kusamvana komwe kwabuka mu MCP momwe akuluakulu ena 5 akudzudzula mtsogoleri wa chipanicho Lazarus Chakwera pa kayendetsedwe ka chipani. Ming’alu idakulanso pomwe Sidik Mia akufuna mpando wa wachiwiri kwa Chakwera umene uli m’manja mwa Richard Msowoya yemwe ndi mmodzi mwa ziphona za MCP zimene zikutsutsana ndi Chakwera.

Koma Chakwera wati mikangano yomwe yakula m’chipanicho siyingaopseze mwayi wake wodzapambana pa chisankho cha mu 2019.

Iye wati akuluakulu a chipani akuyembekezeka kukumana kuti akambirane za msonkhano waukulu wa kovenshoni komwe adindo a kumtima kwa anthu akasankhidwe.

“Chipani chathu ndi chosiyana ndi zipani zina ndipo anthu asawone ngati zomwe zidamveka masiku amenewa zingatigwerule nkhongono,” Chakwera adatero.

Ndipo m’chipani cha Aford, Enoch Chihana, yemwe wakhala akutsogolera chipanicho nthawi yonseyi ndi mkhalakale pa ndale mchigawo cha kumpoto Dan Msowoya akulimbirana utsogoleri wachipanicho.

Msowoya akuti potengera malamulo a chipani, mtsogoleri ndiye kufikira msonkhano waukulu wachipani udzachitike pomwe Chihana akutsutsa izi ponena kuti mtsogoleri ndiye. “Ndine mtsogoleri wachipanichi mpaka mu April pomwe tidzakhale ndi kovenshoni,” adatero Msowoya.

Koma Chihana adati izi ndi nkhambakamwa chabe. “Enawa angotumidwa kuti adzasokoneze basi. Palibe chanzeru chomwe akufuna kuchipani kuposa kugwira ntchito ya omwe awatumawo,” adatero Chihana.

Ndipo ku PP, thengenenge pa maudindo silikutha chichitikireni chisankho cha mu 2014 pomwe mtsogoleri wake Joyce Banda yemwe adali Pulesidenti wa dziko kuchoka mu 2012 mpaka 2014 adanka kunja.

Ena mwa akuluakulu achipanichi adamukira kuchipani cha DPP. Awa ndi monga Ken Msonda yemwe adachoka yekha komanso Christopher Mzomera Ngwira yemwe adachita kuchotsedwa m’chipanicho. Ndipo m’sabata ikuthayi, Uladi Mussa ndi Ralph Jooma—omwenso ndi aphungu a chipanicho—adachotsedwa.

Mneneri wa chipani cha PP Noah Chimpeni wati mikangano siyitanthauza kuti chipani chikutha koma kuti demokalase ikugwira ntchito chifukwa anthu akulimbirana maudindo.

Iye wati chipanicho sichidalingalirebe za kovenshoni koma watsimikiza kuti msonkhanowu udzachitika nyengo ya chisankho isadafike.

Related Articles

Back to top button