‘Timakaonera masewero a mpira’

Masewero a pakati pa Police Secondary School ndi St Paul Private Secondary ku Zomba adzakhala chikumbutso kwa Owen Chaima, kuti adapezerapo nyenyezi yomwe lero wamangitsa nayo woyera.

Zoti masewerowo adatha bwanji, Owen sakumbukanso chifukwa chomwe amakumbukira bwino ndi “Talandila Mwandira” amene pakutha pa masewero adapeza chisangalalo, lero njoleyi ikugonera pachifukwa chake.

Nganganga mpaka imfa: Owen ndi Talandira

Umotu mudali mu 2008 pamene Owen, yemwe ndi goloboyi wa timu ya mpira wamiyendo ya Mbeya City m’dziko la Tanzania adaona dzanja la Mulungu.

“Tonse timakonda masewero ampira, patsikuli tidangopita kukaonera mpira. Basitu kukumana kwake kudali komweko,” adatero Owen.

Pamene masewerowo amachitika, nkhani zosaleka zidali zikukambidwa ndipo maso pa masewerowo adachoka pamene chidwi chidali pa ubwenzi umene Owen amafuna uyambike. Komabe Talandira adali asadachilandire kuti avomere.

Pakutha pa masiku chibwenzi chidayamba ndipo nkhani zatsogolo zidayamba kuphikidwa.

“Inetu mwamunayu ndidamukonda chifukwa cha khalidwe lake lodzichepetsa komaso ndimadziwa kuti adali Mulungu amene adatilumikizitsa,” adatero Talandira yemwe lero ndi mayi Chaima.

Pa 11 November sabata yapitayo, awiriwa adalumbira ku Mount Oliver CCAP ya ku Chilobwe mumzinda wa Blantyre kuti mpaka imfa ndiyo idzawalekanitse ponenetsa kuti kusowa kapena kupeza zachepa kufika powalekanitsa.

Mwambowu udafika penipeni pamene awiriwa adatengera unyinji wa anthu ku Miracle Garden ukutu ndi ku Naperi mumzindawu komwe kudali kumwelera ndi kudya tofewa.

Share This Post