Nkhani

‘2019 ikudetsa nkhawa’

Listen to this article

Chikhulupiliro chapita. Amalawi 28 mwa 100 aliwonse akuti akuona chisankho chopanda mtendere ndi chilungamo chaka cha mawa.

Izi zadziwika potsatira kafukufuku wa nthambi yofufuza za maganizo a anthu pankhani zosiyanasiyana ya Institute of Public Opinion and Research (Ipor).

Kafukufukuyo yemwe adayendetsa ndi akadaulo pa kayendetsedwe ka boma ndi ndale wasonyeza kuti Amalawi ali ndi nkhawa kaamba ka zina mwa zomwe zikuchitika mdziko muno pokonzekera chisankhochi.

“Anthu omwe ataya chikhulupilirowa akuti nkhani za zipolowe, mphekesera zodzabera chisankho, malingaliro okondera ku bungwe la MEC ndi kusayenda bwino kwa zisankho za mmbuyomu ndizo zifukwa,” latero lipoti la kafukufukuyu.

Koma pomwe chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) chadzudzula kutsogoza maganizo otere, zipani zotsutsa zati maganizo a anthuwo ali ndi tanthauzo.

“Zisankho za m’mayiko a mu Africa zimasokonekera chifukwa cha mchitidwe wotsogoza kutaya chikhulupiliro mmalo momasakasaka njira zokonzera zinthu,” adatelo mneneri wa DPP Nicholas Dausi.

Iye adati chofunika nchoti anthu angokhulupilira kuti chisankho chidzayenda bwino basi kuti pasadzakhale kukokanakokana pa zotsatira zachisankhocho.

Mneneri wa chipani cha Malawi Congress (MCP) Maurice Munthali adati nkhawa yachisankho chopanda chilungamo ndi mtendere zidabwera Nyumba ya Malamulo itangokana kusintha malamulo oyendetsera chisankho.

“Kusintha malamulo kuja lidali ganizo la nthambi zosiyanasiyana zomwe zidali zitaona kufooka kwa malamulo oyendetsera chisankho ndiye nkhaniyi itangokanidwa, anthu adataya chikhulupiliro pompaja,” adatelo Munthali.

Iye adati zipani zandale nazo zikuonjeza kunyogodolana pamisonkhano ndi kuchulutsa mawu odzetsa mkwiyo ndi kuyambitsa ziwawa.

“Tikapanda kusintha khalidwe lonyoza ndi kulankhula zodzetsa mkwiyo ndi kuyambitsa phokoso pa misonkhano yathu, tiyembekezere ulendo owawa wa ku chisankho,” adatelo Munthali.

Mneneri wa United Transformation Movement (UTM) Joseph Chidanti Malunga adati akugwirizana kwa thunthu ndi anthu omwe akuwona mdimawa potengera zomwe zikuchitika mdziko muno.

“Taona kangapo konse pakuchitika zofuna kulepheretsa anthu kubwela ku misonkhano yathu, apa akulimbana nafe kuti tisalembetse chipani komanso mukumbuka kuti adatiwotchera galimoto ku msonkhano wa ku Mangochi. Zonsezi anthu amaona,” adatero Malunga.

Kafukufukuyo, yemwe adachitika m’miyezi ya August ndi September 2018, akusonyeza kuti DPP yomwe ili ndi oyitsatira ambiri kumwera ili ndi danga lalikulu lodzapambana chisankho.

Lipotilo lasonyezaso kuti MCP ikubwela pachiwiri ndipo mphamvu zake zadzadzana pa chigawo cha pakati kutsatidwa ndi UTM yomwe mphamvu zawoneka ku mpoto.

MCP kudzera mwa mneneli wake Munthali yatsutsa zoti iyo ili ndi mphamvu mchigawo chapakati chokha ponena kuti chipanichi chidazika mizu mzigawo zina za dziko lino.

“Sitikudelera omwe adapanga kafukufukuyu koma patokha tikuwona kuti talanda malo mzigawo zina. Chitsanzo ndi zotsatira za chisankho chachibwereza cha 2017,” adatero Munthali.

Chipani cha MCP chatchulidwa kuti ndicho anthu ambiri ali nacho chikhulupiliro choti chitha kudzakonza zinthu zomwe zidaonongeka pa kayendetsedwe ka dziko.

Iye adati DPP ndi yolimbikitsidwa ndi zotsatira za kafukufukuyo ndipo yati ilimbikira kukonza zofowoka zomwe kafukufukuyo wayipeza nazo.

Zipani ziwirizi zagwirizana maganizo kuti UTM yangogweramo m’bwalo kaamba koti kafukufukuyo adachitika nthawi yomwe gululi limakhazikitsidwa kumene ndiye lidali n’chikoka.

Malunga adati UTM n’chiwopsezo chachikulu ku zipani za DPP ndi MCP ndipo adati zotsatira za kafukufukuyo zatsimikiza mphamvu ndi kuwopsa kwa UTM.

Related Articles

Back to top button