‘Obwereza MSCE adzionere njira’

Unduna wa zamaphunziro wati siungachite kulembetsa mayeso apadera ophunzira 72 542 omwe adalakwa mayeso a Malawi School Certificate of Education (MSCE) a 2018 monga momwe makolo ndi anawo amalingalirira.

Makolo ena ndi ena mwa ana omwe adalephera mayesowo adauza Tamvani kuti zikadathandiza ana olephera akadalemba mayeso awoawo ogwirizana ndi silabasi yakale yomwe adaphunzira.

Chide: Sizikusiyana kwambiri

Koma mneneri wa undunawu Lindiwe Chide wati ophunzira onse adzalemba mayeso a silabasi yatsopano ndipo kwa omwe sadaphunzire nawo silabasiyi adziwiretu chochita kuti zidzawayendere.

“Palibe kusintha kwakukulu pakati pa silabasi yakale ndi yatsopano ndiye palibe chifukwa cholembetsera mayeso osiyana. Yemwe akuona kuti pali zina zomwe ali mmbuyo, akuyenera kupeza njira yoti azidziwe,” watero Chide.

Iye wati aphunzitsi ndi wokonzeka kusula ana onse obwereza ndi omwe adzalembe mayeso koyamba kuti adzakhonze koma mkulu wa mabungwe omwe siaboma pa za maphunziro Benedicto Kondowe watsutsa mfundoyi.

“Choyamba, aphunzitsi ambiri sadaphunzitsidwe za kaphunzitsidwe ka silabasi yatsopano komanso alibe mabukhu owatsogolera pophunzitsa. Kachiwiri, silabasi yatsopano ndiyodzadza ndi za sayansi zomwe ambiri obwereza sadaphunzirepo,” watero Kondowe.

Iye wati ophunzira ambiri obwereza ndi omwe akudzalemba mayeso koyamba adzakukuta mano m’mayeso chifukwa adzakhala asadakonzekere mokwanira potengera momwe silabasi yatsopano idakhazikitsidwira.

“Mukakumbuka, mabukhu ambiri adachedwa kubwera, ndi nkhani ya sayansiyi, kumafunika zipangizo ngati malabotale omwe m’sukulu zambiri makamaka ma CDSS mulibe. Ndiye ngati akudetsa nkhawa mwana yemwe adaphunzirako zithuzo pang’ono, kuli bwanji yemwe sadaphunzirepo kalikonse,” watelo Kondowe.

Makolo ndi ana omwe alankhula ndi Tamvani ati akadakonda pakadakhala mayeso apadera ochokera mu silabasi yakale oti ana omwe akubwereza adzalembe kenako n’kumapanga ndondomeko yophatikiza ndi ophunzira a silabasi yatsopano.

Jennifer Ngwira wa ku Area 25 yemwe mwana wake adalakwa mayeso a MSCE adati kukakamiza anawo kulemba mayeso a silabasi yatsopano n’kuwapha chifukwa palibe chomwe angadzaphulepo.

“Ngati mwana adalakwa zinthu zomwe adaphunzira, angadzakhonze bwanji zomwe sadaphunzirepo n’komwe? Uku ndiye kufuna kupha tsogolo la ana,” adatero Ngwira.

Mmodzi mwa ana omwe akuyembekezera kubwereza mayeso a MSCE ndipo sadafune kutchulidwa dzina adati sakuona tsogolo lililose mundondomeko yomwe undunawu wakonza.

“Poyamba tinkamva zoti tidzabwerera Fomu 1 zomwe tidakonzekera kale kutsutsa akadzalengeza tsono apa akuti tilemba silabasi yatsopano, si chimodzimodzi n’kubwereza?” adatero iye.

Mwa ana 197 286 omwe adalemba mayeso a MSCE a 2018, ana 124 745 ndiwo adakhonza kutanthauza kuti 72, 542 adalakwa ndipo akuyenera kubwereza ngati ali ndi chidwi chopita patsogolo ndi maphunziro.

Share This Post