Nkhani

Zili bwino—PAC

Listen to this article

Nduna yakale ya zaulimi George Chaponda yamangidwa patatha masiku 43 kuchokera pamene nthumwi kumsonkhano wa Public Affairs Committee (PAC) lidapatsa boma masiku 30 kuti limange ndi kuzenga mlandu ndunayo poyiganizira kuti idachita zachinyengo.

Imodzi mwa mfundo zimene nthumwizo zidamanga pamsonkhano umene udachitika mumzinda wa Blantyre pa 7 ndi 8 June, idali yoti Chaponda amangidwe malinga ndi kafukukufuku amene makomiti a Nyumba ya Malamulo adachita ndi kupeza kuti ndunayo idachita za chinyengo pogula chimanga ku Zambia. Komiti ina imene adakhazikitsa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika idapezanso kuti Chaponda adachita ukapsala.

Chaponda (Kumanja) ndi Tayub kufika kukhoti Lachinayi

Bungwe la ACB Lachitatu lidamanga Chaponda limodzi ndi mkulu wa kampani ya Transglobe Rashid Tayub komanso wapampando wa bungwe loona za malonda a mbewu zosiyanasiyana la Grain Traders Association of Malawi, Grace Mijiga Mhango.

Lachinayi, oyimira Chaponda adapempha bwalo la majisitileti kuti lichotse chikalata choti mkuluyo amangidwe koma bwalolo lidakana pempholo choncho adagonanso m’chitokosi. Mhango adapatsidwa belo Lachitatu.

Ndipo madzulo a tsiku lomwelo, bwalolo lidapereka belo kwa Chaponda ndi Tayub.

Mneneri wa PAC Peter  Mulomole adati akuyembekezera kuti ACB ipitiriza ntchito imene ayiyambayi mpaka kumapeto kuti chilungamo chidziwike.

“Uku ndiko kukhala. Aliyense aziyesedwa ndi mlingo umodzi chifukwa palibe yemwe ali pamwamba pa malamulo. Chiyembekezo chathu tsopano n’choti momwe zateremu, ACB ikoka nkhaniyi mpaka kumapeto,” adatero Mulomole.

Mkulu wa bungwe la Centre for the Development of People (Cedep), Gift Trapence, wati zomwe yachita ACB zaonetsa kuti bungweli layamba kugwira ntchito mosaopsezedwa.

“Uku ndiye timati kukula. Bungwe la ACB siliyenera kugwira ntchito mwamantha kuopa maina. Apa tikuyembekezera kuti zonse ziyenda bwino mpaka chilungamo chioneke,” adatero Trapence.

Mwezi wathawu, Chaponda adanena poyera kuti iye ndi wokonzeka kunjatidwa ngati Amalawi akuona kuti ndiwolakwa koma iye adabwereza kuti akudziwa kuti akufera kuthandiza Amalawi omwe akadafa ndi njala.

Related Articles

Back to top button