Nkhani

‘Smartmatic’ yautsa mapiri pa chigwa

Njira yamakina a makono oyendetsera zisankho otchedw Elections Monitoring Devices (EMD) amene akutchuka ndi dzina la kampani yak u Netherlands imene imawapanga ya Smartmatic yomwe bungwe la zisankho la MEC likuyembekezeka kugwiritsa ntchito pa chisankho cha 2025 yautsa mapiri pa chigwa.

Zipani za ndale zina komanso mabungwe omwe si aboma ena akuti bungwe la MEC lisinthe ganizo lake pa makinawo ndi kutsata njira yomwe yakhala ikugwiritsidwa ntchito pa zisankho za mmbuyomo.

EMD ndi njira ya makono yogwiritsa ntchito pa kalembera, kuwerenga ndikutumiza zotsatira za zisankho koma malingana ndi zipani za ndale monga DPP, Aford, UDF komanso UTM, pali chiopsezo chosokoneza zisankho ndi makinawo.

Bungwe la MEC litalengeza kuti lasankha kampani ya Smartmatic, zipanizo zidapanga msonkhano wa atolankhani komwe zidalengeza kuti sizikufuna kampaniyo ndi makina ake pa chisankho chomwe chikubwerachi.

“Makinawo tikuwakana chifukwa MEC idasankha kampaniyo osakambirana ndi zipani za ndale ngati momwe zimayenera kuyendera. Chachiwiri, kampani imeneyi ili ndi mbiri yosokoneza zisankho kwina komwe idatengedwanso komanso tikuona kuti pali chiopsezo chachikulu chobera zisankho,” adatero Shadrick Namalomba a chipani cha DPP koma amalankhula mmalo mwazipanizo.

Gawo 4 la malamulo oyendetsera zisankho omwe Nyumba ya Malamulo idavomereza mu December 2022, limati bungwe la MEC liziyendera limodzi ndi zipani za ndale pa chilichonse chokhudza zisankho.

Naye mtsogoleri wa chipani cha Aford a Enock Chihana adanenetsa pa msonkhano wa zipanizo omwe udachitikira ku nyumba kwawo kuti sadzalola kuti makinawo adzagwiritsidwe ntchito pa chisankho.

“Akakakamira kudzagwiritsa ntchito makina a Smartmatic, akonzekele kuti akawagwiritsa ntchito ku dambwe,” adatero a Chihana ndipo mawuwo adautsa mkwiyo pakati pa Achewa omwe amatenga dambwe ngati malo awo achinsinsi.

Nawo mabungwe oyima paokha monga Center for Democracy and Economic Development Initiative (Cdedi) komanso Nzika Zokhudzidwa adachenjeza kuti MEC ikapitiriza ganizo la Smartmatic, iwo adzatsogolera zionetsero zotsutsa.

“MEC idziwe kuti zisankho zomwe zikubwera n’za Amalawi ndiye ikuyenera kupanga zomwe Amalawi akufuna osati zomwe ilolo likufuna. Apapa n’zachidziwikire kuti Amalawi sakufuna Smartmatic ndiye MEC isapitirire kugwiritsa ntchito makina amenewo,” adatero mkulu wa CDEDI a Silvestre Namiwa.

Pomwe mtsogoleri wa gulu la Nzika Zokhudzidwa a Bon Kalindo adati: “Sitikufuna makina amenewo a Smartmatic komanso apereke mpata kwa anthu adera oti adzaunike kaundula wa chisankho apo ayi akonzekere zionetsero za dziko lonse.”

Koma pa nkhani yonseyi, mkulu wa bungwe la MEC mayi Annabel Mtalimanja adanenetsa kuti makina a Smartmatic adzagwira ntchito pa chisankho komanso kuti kampani ya Smartmatic ndi yokhayo yomwe idaonetsa khumbo loti makina ake adzagwire ntchito pa chisankho.

“Sikut i tidangowatola pa msewu ayi, nthumwi kuphatikizapo a zipani adapita ku South Africa kukaona momwe makinawo amagwirira ntchito ndiye samakana nthawi yomweyo bwanji,” adatero a Mtalimanja.

Kuonjezera apo, iwo adati makina a Smartmatic atafika ndipo asadayambe kugwiritsidwa ntchito, nthumwi za zipani za ndale zidaitanidwa n’kukaona momwe makinawo azigwirira ntchito koma panthawiyo padalibe yemwe adaonetsa kusakhutira nawo.

Koma atsogoleri a mipingo ina akuti MEC ikuyenera kumvera zofuna za Amalawi kuti chisankho chidzayende bwino koma kutero ndiye kuti MEC ikuyenera kuyambi ranso kaundula watsopano zomwe zingafuneso ndalama zapadera.

Malingana ndi kaundula yemwe MEC idapereka ku zipani kuti zizukute, mwa Amalawi 7.2 miliyoni adalembetsa m’kaundula mwa anthu pafupifupi 11 miliyoni omwe ndi wovomerezeka kudzaponya voti pa 16 September 2025.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Check Also
Close
Back to top button