Polisi yati mitima ikhale mmalo
Mkulu wa apolisi Mayi Me r l y ne Yol amu atsimikizira zipani za ndale ndi mabungwe oima paokha kuti asade nkhawa ndi nkhani ya chitetezo pomwe dziko likulowera ku Chisankho Chachikulu pa 16 September, 2025.
A Yolamu amalankhula izi pa mkumano wa apolisi, zipani za ndale ndi mabungwe omwe lidakonza bungwe losanthula momwe zinthu zikuyendera m’dziko lino la Public Affairs Committee (PAC) mu mzinda wa Blantyre Lachiwir i ndi Lachitatu.

N k h a n i y a i k u l u k u mkumanowo idali yokhudza chisankho ndi zomwe zikuchitika pokonzekera chisankhocho koma uli mkati, mitima idakwera ndipo a mabungwe ndi zipani osiyanasiyana adakhazikika pa nkhani ya chitetezo.
Mabungwe ndi zipanizo zimadzudzula apol i si kuti amakondera mbali ya boma popereka chitetezo komanso pofufuza milandu yokhudza mikangano ya ndale ponena kuti zikakhala zoipira otsutsa, apolisi amaoneka pomwe zikaipira boma, apolisiwo amakhumata.
Poyankha chidzudzulocho, a Yolamu adati sizoona kuti kwa milandu ya mtunduwo, athu omwe adamangidwa komanso milandu yomwe adathana nayo ndi zotsatira zake.
“Chomwetu chingapereke chikhulupiriro kwa Amalawi ndi pokhapokha mutanena kuti ndi milandu ingati ya mtunduw u yomwe idachitika komanso ndi iti yomwe mudathana nayo. Kupanda kupereka zimenezi, chikhulupiriro cha Amalawi chikhalabe chochepa,” adatero a Trapence.
Mkulu wa bungwe la Center for Democracy an Economic Development Initiative (Cdedo) a Silvestre Namiwa adaonjeza kuti pamwamba pa kupereka chiwerengero cha milandu ndi anthu omwe adamangidwa, a Yolamu atchule maina a anthuwo.
“Anthu akufuna muwauze makhoti omwe a kumv a milandu ya zipolowe yomwe yakhala ikuchitika monga aja adakatema anthu ndivzikwanje ku zionetsero ku Lilongwe komanso omwe adaphwetsa matayala ndi kuswa galimoto za aphungu otsutsa ku Nyumba ya Malamulo ndi ndani,” adatero a Namiwa.
Mtsogoler i wa amayi m’chipani cha DPP Mayi Mary Nav icha womwe ada i m i ra c h i pan i c ha DPP adafunsa a Yolamu chomwe chimachitika kuti apolisi azichedwa kufufuza milandu yokhudza otsatira chipani cholamula.
Mayi Jessie Kabwi ra omwe ndi mneneri wa MCP adap empha kuti apolisi afufuze nkhani zonse za zipolowe za ndale zomwe zakhala zikuchitika ndi gwero lake.
Poyankha, a Yolamu adati: “Apolisi adafufufza nkhani zonse. Mbali ya boma ndilo limachitiridwa mtopola kwambiri.” Ndipo adawonjezera kunena kuti pa nkhani ya chisankho, chitetezo chili kale ndi ndondomeko ndipo anthu asade nkhawa iliyonse.
Pa k a t i p o, p a k h a l a pakuchitika zipolowe za ndale zosiyanasiyana zomwe zikachitika, zipani zotsutsa zimaloza zala boma ndipo boma lakhala likudzudzula kuti otsutsawo amapangira dala ndicholinga choti aziipitsa boma.



