Nkhani

Amanga oba zitsulo pa mlatho

Apolisi m’boma la Mulanje atsekera m’chitokosi abambo anayi powaganizira kuti adaba zitsulo za pa mlatho wopezeka m’dera la kummwera cha kummawa kwa boma la Mulanje.

Mneneri wa polisi ya Mulanje a Innocent Moses atsimikiza kuti amanga a Peter Mangombo a zaka 29, a Jimmy Yoana (24), a Smart Jeseman, (22) ndi a Bright Lumbe (26).

A Moses, adati apolisi adalandira uthenga kuchokera kwa akufuna kwabwino woti mchitidwe wa ukamatulewo wakula kuderalo. Ndipo poyamba, iwo adakamang’ala kwa phungu wa ku Nyumba ya Malamulo kuderalo, Mayi Naomi Phiri n’cholinga choti mchitidwewo utheretu.

Koma amunawo podziteteza, adatchula phunguyo kuti ndi amene ankawatuma kuti azikaba zitsulozo.

A Moses adafotokoza kuti pa 1 June 2025, cha kumasana, a Phiri, adalandira lamya kuchokera kwa mfumu Namunda kuti anthu ena adabwera ndi kutenga zitsulo za pa mlathowo nazikweza m’galimoto yaikulu ya Isuzu yomwe nambala yake idali MJ 10590.

“Mosakhalitsa, phunguyo adalumikizana ndi achitetezo a m’mudzimo kuti akalande katunduyo ndipo mwamwayi, iwo adakwanitsa kulanda zitsulozo pamodzi ndi galimotoyo. Kenaka adawatengera ku polisi kuti akafotokoze cholinga chawo pochita za upanduzo,” adatero a Moses.

Tsono apolisi akulangiza anthu m’bomalo kuti azichita machawi komanso kunena msanga ku polisi yomwe ali nayo pafupi pamene akuwakaikira ena kuti akuba kapena akusakaza katundu wa boma. Iwo adati kuchita zoterezi msanga zidzathandiza kuteteza miyoyo yawo ngakhalenso katundu wawo.

Amuna omwe agwidwawo amachokera m’midzi ya Machokola, Themba ndi Njema, yomwe ili m’dera la T/A Mabuka, m’bomalo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button