Achenjeza maboma 23 za nyengo ya el nino
Nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi ya DoDMA yachenjeza kuti ulosi woyamba wa nyengo ya mvula ya chaka chino wasonyeza kuti maboma 23 mwa maboma 28 m’dziko muno adzakhudzidwa ndi ng’amba yobwera ndi mphepo ya El-Nino.
Ena mwa maboma omwe akuyembekezeka kudzakhudzidwa ndi a Balaka, Blantyre, Blantyre City, Chikwawa, Chiradzulu, Dedza, Dowa, Kasungu, Lilongwe City, Machinga, Mangochi, Mchinji, Mulanje, Mwanza, Mzimba, Neno, Nkhata Bay, Nkhotakota, Nsanje, Ntchisi, Phalombe, Thyolo ndi Zomba.

Malingana ndi ulosi wa nthambi ya za nyengo, maboma a kummwera monga Blantyre, Chikwawa, Nsanje, Mulanje, Thyolo, Phalombe, Mwanza, Neno, Balaka, Mangochi, Ntcheu, ndi Chiradzulu adzakhala ndi ng’amba yowopsa komanso madzi osefukira.
Ulosiwo wati maboma a m’chigawo Chapakati monga Ntchisi, Dowa, Lilongwe ndi Dedza adzakhala ndi ng’amba yapakatikati komanso adzayembekezere kulandira mvula yambiri.
M’maboma a Kumpoto, komwe nthawi zambiri kumakhudzidwa kwambiri ndi ngozi zadzinja, makamaka kusefukira kwa madzi, ulosi wa nthambi ya za nyengo wasonyeza kuti sikudzakhudzidwa kwambiri makamaka ndi ng’amba.
Lipoti la mkumano wa akadaulo, omwe udakonzedwa ndi bungwe la International Food Policy Research Institute (Ifpri) ndi nthambi yokonza zitukuko za boma ya National Planning Commission (NPC) pa 30 June 2026 lidaunikira kuti ndi pofunika kukonzekera nthawi yabwino.
“Tikakonzekera nthawi yabwino ndiye kuti tidzakwanitsa kuthana ndi vuto lomwe latilunjikali koma tikalephera kukonzekera, zotsatira zidzakhala zowawa osati kwa alimi okha komanso ku boma chifukwa lidzakhala ndi chintchito chothimitsa moto,” lidatero lipotilo.
Kadaulo pa za ndondomeko za malimidwe a Tamani Nkhono-Mvula adati, nyengo iliyonse imakhala ndi njira zake zokonzera, makamaka vuto likaonekera patali ndipo kukonzekera kwayenda bwino.
“Apatu tikuyenera kunjenjemera ndi nkhani ya El-Nino komanso tikuyenera kudzitenga odala chifukwa tadziwa nthawi yabwino ndipo tili ndi nthawi yambiri yoti titha kukonzekera mokwanira n’kudzapulumuka,” adatero a Nkhono-Mvula.
Pa mkumano wa aphungu a Nyumba ya Malamulo, womwe udatha sabata zitatu zapitazo, aphungu adafunsa boma kuti lilongosole bwino chomwe chikuchitika pokonzekera mphepo ya El-Nino yomwe umboni umasonyeza kuti imachepetsa zokolola kaamba ka khalidwe lake.
Mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma a Simplex Chithyola-Banda adati chetechete akhoza kumapereka chithunzithunzi choti zinthu zili bwino ndipo alimi akhoza kudzadzidzimuka nkhwangwa ya El-Nino ili m’mutu.
“Tikufunika kuti tiziwauza alimi zoona zomwe zikuchitika zokhudza mphepo ya El-Nino chifukwa tikangokhala chete aziona ngati zonse zili bwino pomwe tikudziwa kuti zinthu sizilibwiinokonse ayi. Tulukani poyera ndi kulongosola zomwe zikuchitika,” adatero a Chithyola-Banda.
Polankhula kudzera pa Intaneti pa msonkhano wa nduna zoona za malimidwe za m’maiko a mu Africa, wokambirana za El-Nino mwezi wa July 2026, nduna ya za ulimi mayi Roza Mbirizi adati dziko la Malawi lili patsogolo ndi zokonzekera kulimbana ndi El-Nino.
“Tidapanga ndondomeko yolimbana ndi vutoli. Tikhala tikugwira ntchito ndi nthambi zosiyanasiyana, koma pa mtima pa zonsezi, pali komiti ya nduna za boma yomwe idakhazikitsidwa ndi a Pulezidenti a Peter Mutharika kuti izitsogolera,” adatero a Mbirizi.



