Ngozi za sitima zagundika
Kusowa kwa zizindikiro zosonyeza pomwe sitima ikudutsa, kugulitsa malonda mphepete mwa njanji ngakhalenso kufuna kudzipha, ndi zina mwa zimene zikukolezera ngozi za sitima m’dziko muno.
Izi tapeza kuchokera m’kafukufuku wathu pa malo amene njanji zimadutsa msewu ku Limbe, Magalasi ndi Area 1 mu mzinda wa Blantyre; kwa Nkhwazi, Kamwendo ndi pa Boma ku Mchinji ngakhalenso pa Boma ku Salima.

Koma ngakhale akuluakulu akulephera kunena molongosoka chiwerengero cha ngozizi, zikunka zichullukira.
Sabata yatha a Emmanuel Chipeta a zaka 50 adafa pamene galimoto yawo ya mtundu wa Toyota Harrier idagunda sitima m’mudzi mwa Kalonga kwa Senior Chief Kalonga. Mnzawo Yazidu M’balaka wa zaka 32 akadali m’chipatala pomwe iwo sadamve hutala ya sitima imene idagunda galimoto yawoyo.
Ndipo sabata yatha yomweyo, thilaki ina idagunda galimoto zina zisanu zimene zidaima kudikira sitima kuti idutse pa Magalasi pomwe mkulu wina, a Innocent Zakeyu adagundidwa ndi sitima pa Area 1 ku Machinjiri.
Ku Mchinji, komwe sitima yakhala nthawi yaitali isakuyenda, ngozi yomaliza idachitika m’chaka cha 2015 pomwe mwana amene adali ndi zaka 7 adaduka miyendo sitima itamugunda. Koma pano, dandaulo lilipo chifukwa akunyalanyaza pomwe ena akuotha moto mu njanji kumene.
Nkhani za anthu ngakhalenso galimoto kuchita ngozi ndi sitima zakhala zikuyala nthenje m’dziko lino.
Senior Chief Kalonga adati pakafunika kufalitsa uthenga kwambiri kuti zoyala malonda mu njanji zithe ngakhalenso kunyalanyaza.
“Zikundikhudza ndipo ndayankhula mokwana za ngozi za sitima kuno kwathu, kuphatikizapo yomwe yangochitika kumeneyi. Si kale ayi, wina adamenya makolo ake ndipo adachita kutsanzika kuti ndikukagundana ndi sitima ndipo adakadziponyadi.
“Kunena za misika ya mu njanji ndiye osanena. Apolisi akadabwerapo n’kutola anthu angapo kuti mchitidwewu utheretu. Ngozizi zankitsa ndipo zikufika poopsa,” idatero mfumuyo.
Pophera mphongo, a Fatsani Chikaoneka adati nthawi zinanso pa misika ya mu njanjiyi amagulitsa mowa zomwe zikuonjezera chiopsezo cha ngozi. “Akugulitsa bibida komanso uthenga wa momwe anthu angasamalire kuti apewe ngozi za sitima siukukhala wokwanira,” adatero iwo.
Malinga ndi kafukufuku wathu, malo onse amene njanji zimadutsa msewu ku Blantyre, Salima, Mchinji ndi Balaka palibe magetsi amene amayaka ngati sitima ikubwera. Malinga ndi oyendetsa galimoto amene tacheza nawo, izi ndi zoopsa chifukwa sadziwa ngati kukubwera sitima kufikira ili pafupi.
A Emmanuel Cosmas omwe amayendetsa minibasi kuchoka mu Limbe kupita kwa Kachere ndipo nthawi zambiri amadutsa njanji adati poyamba nyale zinkagwira ntchito ndipo ankadziwa msanga kuti aime koma pano amangozindikira sitima yafika.
“Nyalezi zidazima ndipo timangozindikira sitima ili pambalipa. Izi zikuika pa chiopsezo miyoyo yathu komanso anthu omwe timatenga chifukwa n’kovuta kudziwa kuti sitima ikubwera,” atero iwo.
Nawo a Simeon Maloya, omwe amachita bizinesi ya kabaza ku Limbe ati oyendetsa sitima amaimba hutala atafika kale malo amene njanji imadutsa msewu, zomwe zimachititsa kuti atutumuke ndi kuchita zinjenje.
Iwo adati: “Zikadakhala bwino akadati aziimbira patali chifukwa akamaimba pafupi timachita pakalapakala zimene zingadzetse ngozi.”
Malinga ndi a Felix Mankhwazi omwe amayendetsa kabaza pakati pa Kamwendo ndi Kapiri ku Mchinji, pa mbali pa kusoweka kwa nyali zochenjeza anthu ngati sitima ikubwera palibe zikwangwani zosonyeza kuti njanji ikudutsa msewu.
“Anthu ena amaba zikwangwani kuti akonze makasu mpaka pa Nkhwazi palibiretu zikwangwanizo. Pa Kamwendo ndiye kachikwangwani n’kakang’ono. Akadaika chachikulu kwambiri,” adatero iwo.
Mneneri wa kampani yoona za njanji ya Central East Africa Railways a Wezi Kalua ati kuba zikwangwani ngakhalenso kuononga nyalizi kukuonjezera ngozi za sitima zomwe ndi zopeweka ngati anthu atsatira malamulo.
“Tikukonza zoti zipangizozi zibwerere ndipo tayamba kale kuchita izi m’chigawo cha kummwera pofuna kupewa ngozi,” adatero iwo.
Koma a Kalua adati sanganene kuti ngozi zokhudza sitima zikuchuluka motani.
Chimodzimodzinso mneneri wa apolisi m’dziko lino a Alfred Chmthere ndinso mneneri wa nthambi yoona za misewu ya Roads Authority a Lawrent Kumchenga adati sangalankhulepo za chiwerengero cha ngozi za sitima.



