Nkhani

‘Abambo zawakanika, yesaniko amayi’

Listen to this article

Bungwe lomwe likumenyera kuti amayi akhale m’maudindo la Ligowe Community Development Organisation (Licodo) lamemeza anthu a boma la Neno ndi Mwanza kuti ayesereko kuvotera amayi.

Mkulu wa bungwelo, Henry Machemba adati chidwi chawo nkulimbikitsa amayi m’mabomawo kuti apikisane nawo m’maudindo a khansala ndi phungu wa nyumba ya Malamulo.

Machemba adati amayi akudziwa mavuto omwe anthu akumudzi amakumana nawo choncho n’koyenera kuti akhale m’maudindo osiyanasiyana a ndale.

“Tithandiza amayi pa zinthu zambiri kulemba manifesto awo ndi kulankhula pagulu. Tikufuna mipando yambiri ya khansala ndi phungu ipite kwa amayi chaka chamawa,” adatero.

Naye mkulu wa bungwe lophunzitsa anthu zaufulu wawo la National Initiative for Civic Education (Nice) Trust m’boma la Mwanza, Kumbukani Kalulu adati bungwe lake lipitiriza kuuza anthu za kufunika kovotera amayi pamipandoyo.

Mmodzi mwa amayi omwe akufuna kudzapikisana nawo pa uphungu ku dera lapakati m’boma la Mwanza, Lucy Mponda Kampezeni adapempha anthu m’dziko muno kuti avotere amayi.

Polankhula Lachiwiri pamene amakonzekera mpikisano wachipululu wa chipani cha UTM, Kampezeni adati anthu ayesa amuna pa maudindowo choncho n’kofunika kuyesanso amayi.

“Abambo akhala aphungu m’boma la Mwanza kuyambira pamene tidavomereza ufulu wa zipani zambiri.  Koma pali zambiri zomwe sizikuyendabe. Ndikadzasankhidwa, ndidzayesetsa kukonza zinthu,” adatero.

Mwazina, Kampezeni adati adzabweretsa mijigo chifukwa amayi a dera lake akuvutika chifukwa chosowa madzi. n

Related Articles

Back to top button