Nkhani

Achenjeza boma zoimitsa Admarc

Bungwe la ogula katundu la Consumers Association of Malawi (Cama) lati boma lalakwitsa kuimitsa ntchito za kampani yake ya Admarc panyengo yomwe ntchito za kampaniyo zikufunika kwambiri.

Nduna ya zamalimidwe a Lobin Lowe adalengeza Lachitatu kuti boma laimitsa ntchito za Admarc ndipo ogwira ntchito ku kampaniyo auzidwa kuti asapezeke m’maofesi a kampaniyo osaitanidwa.

Koma mkulu wa Cama a John Kapito ati pali njira zambiri zomwe boma likadatha kugwiritsa ntchito pothana ndi mavuto omwe akuchitika kukampaniyo omwe apangitsa boma kuimitsa ntchito zake.

“Apapa tikulowera ku nyengo yovuta yomwe anthu dziko lonse akufuna chimanga koma iwo akuti angotsegulako misika ina komwe kukufunika chimanga kwambiri, mlingo woti kukufunika chimanga ndi koti amutenga kuti,” atero a Kapito.

Iwo atinso boma silingayembekezere kuti anthu omwe liyitanewo angagwire ntchito moyenera pozindikira kuti anzawo akungokhala m’makomo mwawo koma akulandira malipiro chimodzimodzi.

A Kapito achenjezanso kuti zomwe boma lapangali zipangitsa kuti mavenda apezerepo danga nkuyamba kugulitsa chimanga chawo mobera Amalawi zomwe zingapangitse kuti njala ukule m’dziko.

Koma m’mawu awo a Lowe adati angoimitsa zina mwa ntchito za Admarc pomwe zina monga kugulitsa chimanga zizipitirira m’madera ena omwe unduna wawo waona kuti kulibe chakudya chokwanira.

Kuonjezera apo, a Lowe adati onse ogwira ntchito ku Admarc akapume ndipo okhawo omwe aitanidwenso ndiwo ali ololedwa kupita kuntchito pomwe ena onse sakuloledwa kutero.

Iwo adati boma lapanga izi chifukwa cha mavuto omwe akusokoneza ntchito za kampaniyo ndipo boma likufuna kuti likonze mavuto onsewo kuti kampaniyo iyambirenso kugwira ntchito zake molondola.

“Taona kuti Board ya Admarc ndi akuluakulu a kampaniyo amazondana kwambiri, ndalama za kampani sizioneka bwino momwe zimayendera, kumawoneka mawanga aziphuphu komanso ena amalembedwa ntchito mosatsata ndondomeko,” adatero a Lowe.

Andunawo adati kampani ya Admarc ili ndi zolinga zomwe idakhazikitsidwira monga kukweza chuma chaboma, kupatsa alimi chiyembekezo cha msika okhazikika komanso kuonetsetsa kuti mitengo ya mbewu ikukhazikika pomwe boma lakhazikitsa.

Ogwira ntchito ku kampani ya Admarc akhala akuwopseza kuti anyanyala ntchito potsatira mikangano ndi kusemphana pa akuluakulu a Board ndi oyendetsa kampaniyo zomwe zidapangitsa kuti kampaniyo isinthe oyitsogolera kanayi mzaka ziwiri.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button