Nkhani

Zipani zina sizikukhutira ndi madera a aphungu atsopano

Listen to this article

Zipani zina za ndale m’dziko muno zati sizikukhutira ndi momwe malire atsopano a madera a aphungu ponena kuti maganizo awo pakagawidwe ka malire atsopanowo sadagwiritsidwe ntchito.

Izi zikutsatira m’ndandanda watsopano wa madera a aphungu womwe bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) latulutsa womwe waonjezereka ndi aphungu 36.

Asanafike kovota Amalawi ayenera kudziwa malire

Wolankhulira chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) pa nkhaniyi a Bright Msaka ati chipani chawo sichingaikire kumbuyo malire atsopanowo pa zifukwa zikuluzikulu ziwiri.

A Msaka ati pambali pa chifukwa choti maganizo a chipanicho sakuoneka pa mndandandawo, DPP ili ndi nkhawa kuti aphungu oonjezerawo angonkitsa patsogolo mavuto a zachuma omwe alikale mdziko muno.

“Aphungu 193 ndi wokwanira m’dziko muno. Tazungulirani m’maiko ena omwe ndi akuluakulu kuposa Malawi mukaone kuti ali ndi aphungu angati. Zambia mwachitsanzo imaposa Malawi kasanu n’kawiri koma kuli aphungu 150 basi tsono ifeyo tikufunranji kuzunza Amalawi,” adatero a Msaka.

Iwo ati ngati pali ndalama zosowa nazo chochita, boma likadangolemba ntchito aphunzitsi, a zaumoyo ndi apolisi omwe akugwira ntchito ya kalavulagaga kaamba kachiwerengero chawo chochepa.

“Sitinganame kuti aphungu omwe alipo kale 193 akulephera ntchito ayi. Ntchito akugwira bwinobwino moti mukatifusa ngati chipani cha DPP, ganizo limeneli sitikugwirizana nalo,” atero a Msaka.

Nawo a Yeremiah Chihana a Alliance for Democracy (Aford) ati malire atsopanowo akangoutsa mkangano ku Nyumba ya Malamulo ndipo chipani chawo sichingavomereze malire atsopanowo.

“Mukaunike bwinobwino mndandandawo ndipo mukaona kuti madera ambiri apita m’chigawo cha pakati pomwe kumpoto ndi kummwera kwapita ochepa chabe. Chipani cha Aford sichikavomereza malire amenewo,” atero a Chihana.

Koma mlembi wamkulu wa chipani cha United Democratic Front (UDF) a Kandi Padambo ati chipani chawo chikaona ngati maganizo awo adagwira ntchito ndipo ngati adagwira ntchito, chipanicho chilibe mangawa.

“Chomwe ife tikudziwa nchoti a MEC adafunsa maganizo ku zipani komanso mabungwe ena okhudzidwa ndiye ngati adatsatira maganizo a anthuwo podulanso malirewo ife tilibe nazo vuto,” atero a Padambo.

Mlembi wamkulu wachipani cha UTM a Patricia Kaliati ati chipani chawo chakhala chikugwira ntchito limodzi ndi bungwe la MEC pogawanso malirewo kuyambira pachiyambi ndiye sakuyembekezera kusintha kulikonse.

“Sitingamalankhule lero chifukwa takhala tikugwira ntchito limodzi ndi MEC pankhani imeneyi kuyambira pomwe ntchitoyo imayamba ndiye sindikuyembekezera kuti pangakhale kusintha kulikonse,” atero a Kaliati.

Gawo 76 (2) la malamulo limapereka mphamvu ku bungwe la MEC lodulanso malire kuti chiwerengero cha anthu m’dera la phungu lililonse chizidziwika kuti anthu oyenera kulembetsa n’kudzaponya voti chisamasiyane.

M’chaka cha 1964 pomwe Malawi amalandira ufulu wodzilamulira, dziko lino lidali ndi aphungu 53 kenako adakwera kufika pa 63 m’chaka cha 1973.

Mchaka cha 1983, aphunguwo adafika pa 101kenako 112 m’chaka cha 1987 ndipo mu 1992 pomwe ulamuliro wa zipani zambiri unkqbwera, aphunguwo adafika 141ndipo mu 1994, aphunguwo adafika 177 kenako n’kudzafika 193 mu 1998.

Related Articles

Back to top button