Nkhani

Akana kulemba UTM

Akatswiri pa nkhani za ndale ati mlembi wa zipani sadalakwitse pokana kulemba UTM ngati chipani m’dziko muno.

Wachiwiri kwa mlembi wa zipani Chikumbutso Namelo adakana kulowetsa m’kaundula wa zipani gulu la United Transformation Movement(UTM) lomwe likutsogoleredwa ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Saulos Chilima.

Mtsogoleri wa UTM: Chilima

M’chikalata chopita ku UTM kuchokera ku ofesi ya mlembiyi, Namelo adakana kutero chifukwa gululo lidapempha kugwiritsa ntchito dzina la UTM mmalo mwa dzina lonse la United Transformation Movement.

M’kalatayo Namelo adati kugwiritsa ntchito dzina la UTM nkungofuna kubalalitsa ofesi ya mlembiyi chifukwa palinso kale chipani china chotchedwa United Transformation Party (UTP).

Ndipo posakhutira ndi chiganizochi gulu la UTM latengera nkhaniyi ku bwalo la milandu kuti awunike bwino malinga ndi mneneri wa chipanich Joseph Chidanti Malunga.

Koma poperekapo maganizo ake, katswiri pa nkhani za ndale wochokera pasukulu ya ukachenjede ya University of Livingstonia (Unilia) George Phiri adagwirizana kwatunthu ndi ofesi ya mlembi wa zipani kuti kulowetsa mkaundula wa zipani dzina la UTM kukadabweretsa chipwirikiti.

Phiri adati vuto lagona poti nthawi zambiri m’kaundula mumafunika kulowa dzina lonse osati lachidule ayi popangira zokudza pa mawa monga kumangidwa kapena kumanga ena.

“N’chifukwa chokwanira kusawalowetsa m’kaundula chifukwa kwa mlembi wa zipani kukhonza kukhala UTM, iwo kunjako n’kumagwiritsa ntchito United Transformation Movement zomwe zikhonza kubweretsa chisokonezo,” adalongosola motero Phiri.

Iye adati koma vutoli ndi laling’ono ndipo likhonza kukonzedwa mosavuta posagwiritsanso ntchito mabwalo a milandu.

“Ngakhale sindine loya, ndikhonzabe kunena kuti amangoyenera kukhala pansi ndi kuunikanso dzinalo ndi kukonza pali vutopo ndikukaperekanso zikalata zina chifukwa kubwalo la milandu kukhonza kungochedwetsa zinthu,” adatero Phiri.

Pogwirizana ndi Phiri naye Chimwemwe Tsitsi yemwe ndi mphunzitsi kusukulu yaukachenjede ya Polytechnic adati zifukwa zomwe adapereka mlembi wa zipani zidali zomveka bwino potengera malamulo a dziko lino ndi zovuta kulembetsa chipani chomwe chili ndi dzina lofananilako ndi chomwe chidalembetsedwa kale.

“Sitikudziwa kuti a UTM adaganizapo bwanji chifukwa pachiyambi adauza Amalawi kuti aphatikizana ndi chipani cha UTP chomwe mtsogoleri wake ndi Newton Kambala ndipo angochotsa P ndikuikapo M. Koma pano tikuona akukalembetsa ngati UTM,” adadabwa Tsitsi.

Iye adati gulu la UTM likuyenera kukhala pansi n’kuunikapo bwino komanso kupeza upangiri kwa akatswiri amalamulo pa nkhani ya dzinali.

“Akuyenera kupanga izi mwamsanga chifukwa nthawi yawathera kale,” adalongosola Tsitsi.

Ngakhale adaonjezera kuti gulu la UTM likhonza kuona kuvuta kusintha dzina chifukwa cha katundu monga galimoto ndi zovala zomwe zalembedwa m’dzinali ndipo kusinthaku kungakhale kodula.

Related Articles

Back to top button