Nkhani

Kusamvana pa zochotsa fizi

Listen to this article

Ganizo la boma lochotsa fizi pa maphunziro m’sukulu za sekondale ladzetsa chisokonezo m’sukulu zaboma zina pomwe ophunzira ena akukana kulipira fizi ponena kuti boma lachotsa fizi.

Sabata zitatu zapitazo, boma lidalangiza mahedimasitala kuti asatolere ndalama za sukulu fizi, yomwe ndi K500. Ndipo Lachwiri, Unduna wa Maphunziro udalengeza kuti ophunzira asamalipire fizi komanso K500 yochitira zitukuko zosiyanasiyana pasukulu—General Purpose Fund. Koma undunawo udati ophunzira apitiriza kulipira ndalama za malo ogonera pasukulu.

Ophunzira m’sukulu za sekondale sazilipira fizi

Izi zadzetsa chisokonezo pakati pa makolo ndi ophunzira ena omwe akukana kulipira kalikonse kusukulu. Pofuna kumasula thumba la tambe, sukulu zina zikuchititsa misonkhano ya ophunzira ndi makolo kuti athetse mpungwepungwe womwe wabadwa.

Mphunzitsi wamkulu ku Mdeka m’boma la Blantyre, Leo Munyopowa akuti sabata ikudzayi akonza msonkhano wa makolo kuti awafotokozere chimene boma lachotsa.

“Makolo ena akukana kupereka ndalama ponena kuti boma lachotsa fizi, ndiye tangoitanitsa msonkhano wa makolo kuti tiwafotokozere tokha,” adatero Munyopowa.

Chimangeni Gaso wa m’boma la Dedza ndipo amalipirira ophunzira 7, adati kumenekonso padali kusamvana kuti makolo asunge ndalama kenaka boma lidzaitanitsenso.

“Koyambirira zidavuta, ana amadabwa pamene amabwezedwa. Chifukwa cha ichi, tidapita kusukuluko kuti akatifotokozere chenicheni chimene boma lachotsa,” adatero.

Koma nduna ya zamaphunziro Bright Msaka yati kutsatira thandizo lomwe boma lalandira la K6.7 biliyoni kuchokera ku America, ilo laganiza zochotseratu fizi.

Msaka adati kuyambira pa 1 January chaka chamawa, sukulu zauzidwa kuti zisadzatolerenso ndalama yamabuku (textbook revolving fund) yomwe ndi K250, ndalamayi imaperekedwa pa chaka kamodzi.

Izi zikutanthauza kuti kuyambira January chaka chamawa, ophunzira adzilipira ndalama yogonera ngati akugonera pasukulupo ndi zina zoyendetsera sukulu.

Nduna ya zachuma, Goodall Gindwe adati K6.7 biliyoni ndi ndalama yambiri kuposa yomwe boma limalandira m’sukulu ophunzira akalipira zimene lachotsazo.

“Kuchotsa kwa ndalamako sizikhudza boma chifukwa ndalama talandirayo ndi yambiri komanso igwiritsidwa ntchito kumanga sukulu zina,” adatero Gondwe.

Koma mkulu wa bungwe loona zamaphunziro la Civil Society Education Coalition (Csec), Benedicto Kondowe ganizoli ladza modzidzimutsa zomwe zingabweretse mpungwepungwe.

“Ili ndi ganizo la ndale lomwe silingatipatse chilimbikitso. Taona mavuto ochuluka ndi sukulu za pulaimale zaulele zomwe boma lidakhazikitsa, apapa amayenera ayambe aunguza bwino asadabwere ndi ganizoli,” adatero Kondowe.

Komabe anthu ena ndi okondwa ndi ganizoli. Masida Mhango wa m’mudzi mwa Wiskematumbo kwa mfumu Mwahenga m’boma la Rumphi adati chaka chatha, adalephera kuphunzitsa mwana wake chifukwa adalibe ndalama.

“Chaka chatha mwana wanga wa Folomu 3 pasukulu ya Ng’onga adatha chaka chonse wosapita kusukulu chifukwa chosowa ndalama. Izitu zidachitika chifukwa ulimi sudayendenso. Apa ndiye kuti boma laganiza,” adatero. Steven Pembamoyo ndi Martha Chirambo athandizira.

Related Articles

Back to top button