Akana tsankho pa maphunziro
Ophunzira olumala apitirira kukumana ndi mavuto kaamba koti apatsidwa ndalama zochepa mu bajeti ya 2021/22 poyerekeza ndi alunga.
Gulu la akadaulo a za maphunziro la Link for Education Governance (LEG) lati wophunzira aliyense wolumala wapatsidwa K170 pamene walunga walandira K55 000.
Izi zili mu lipoti lomwe LEG yatulutsa ndipo yasinidwa ndi mlangizi wake a Limbani Nsapato, komanso mkulu wake a Davemonie Sawasawa.
Nduna ya zachuma a Felix Mlusu idalengeza kuti bajeti yonse ya maphunziro ndi K327.3 biliyoni, koma mwa ndalama K33.9 miliyoni ndiyo yapita ku nthambi yazaulumali.
Izi zikutanthauza kuti pa K100 iliyonse olumala alandira 10 tambala.
Lipotilo likuta zoterezi ndizo zimadzetsa kusiyana pakati pa maphunziro a olumala ndi a alunga.
“M’dziko muno ophunzira alipo pafupifupi 6 miliyoni, olumala alipo 200 000.
“Mwa ophunzira olumala, 186 501 ali ku pulayimale, 880 ali ku sekondale pamene 137 ali m’sukulu zaukachenjedwe za boma.
“Kuchepa kwa chiwerengero cha ophunzira olumala kukuchitika kaamba kosawalabadira,” latero lipotilo.
Lipotilo lati kuti maphunziro a olumala apite patsogolo pakufunika K500 miliyoni yogulira zipangizo zophunzitsira, K30 miliyoni yophunzitsira aphunzitsi 2 000, K15 miliyoni yophunzitsira alezi 800, komanso K40 miliyoni yophunzitsira aphunzitsi a ku pulayimale ndi ku sekondale ukadaulo ophunzitsira olumala.
A Nsapata adati n’zomvetsa chisoni kuti mwa zofunika zonsezi boma langopereka K33.9 miliyoni yokha m’malo mwa K585 miliyoni.
“Kauniuni wathu akuonetsa kuti ikadakhala K1 biliyoni, boma likadakhala ndi mwayi wolemba aphunzitsi owonjezera 16 611 omwe ali ndi ukadaulo wa m’mene angaphunzitsire ophunzira olumala,” iwo adatero.
Kadaulo wa zamaphunziro, a Benedicto Kondowe, adati vuto n’kusaikapo mtima.
Iwo adati n’zodabwitsa kuti ngakhale maphunziro adasokonekera chaka chatha chifukwa ndalama zapadera zomwe aphunzitsi adapempha kuti azilandira kaamba koti korona ikuika miyoyo yawo pachiopsezo, m’bajeti ya chaka chino ndalamazo mulibemo.
“Izi zikusonyeza kuti boma silidaphunzirapo kanthu pa zomwe zidachitika mmbuyomu,” adatero a Kondowe.
A Michael Kaiyatsa, mkulu wa bungwe la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), adzudzula boma chifukwa chatsankho.
Iwo adati munthu aliyense ali ndi ufulu wofanana ndi mnzake ndipo palibe yemwe ali ndi mphamvu zopondereza ufulu wa wina.
“Ngakhale pa maphunziro, ufulu wa olumala ndi alunga ndi wofanana. Choncho ndalama zomwe walunga walandira, wolumala alandirenso zomwezo,” adatero a Kaiyatsa.
Aphungu a Nyumba ya Malamulo akukambiranabe bajetiyo ndipo a Nsapato ali ndi choyembekezo choti bajeti ya olumala iwunikidwanso bwino.