Akundizunza ku chikamwini
Azakhali,
Ndine mayi wa zaka 24. Ndidakwatiwa ndi mwamuna yemwe ndidamukonda, ndilibe naye mwana chifukwa nditatenda pathupi, mimba idapita malo wosokonekera ndiye adaichotsa.
Mwezi wa November 2022 munthu ananditenga timakhala limodzi ndi apongozipa puloti imodzi koma nyumba zosiyana. Nyumba yathu inalumikizana ndi shopu ndiye anthu akamadutsa kupita ku shopu amadzera pa balaza pa nyumba yathuyi. Ndakhala ndi kuwauza amuna anga kuti atseke chitseko chimenechi amakana. Zinafika poti ndinangozisiya.
Kukhala pakhomo pa apongozi palibe vuto. Chomwe chikundivuta kwambiri n’choti apongozi anga samandifuna ndipo samandiyankhula. Kawirikawiri kumangokhala milandu yokhayokha basi.
Ndikamuuza mwamuna wanga, palibe chomwe amachita. Mumadziwa ukakwatiwa ndi mamuna woti amakhala m’khwapa mwa mayi ake. Zimakhala zovuta kuti akonze zinthu.
Tsiku lina kunabwera mlongo wake wa mwamuna wanga. Analankhula zosakhala bwino. Akuti ndilibe khalidwe ndipo sindimawathandiza.
Komatu ine ndimayesetsa kuphika, kutsuka mbale, kusesa ndipo kugwira china chilichonse pakhomo pawo. Ndikatha ndi pamene ndimagwira ntchito za pa khomo panga.
Alamuwo anandiuza kuti ndinyamule katundu wanga ndizipita kwathu. Ine ndidanyamuka kumapita kwa mchemwali wanga. Ndidawadziwitsa ankhoswe ndipo tidakamba nkhani, koma amaiwa anakaniratu kuti sangakhala pamodzi ndi ine.
Mwamuna wanga naye anapanga chiganizo choti sakundifunanso ukwati.
Ine mwamunayu ndimamukonda kwambiri ngakhale alibe china chilichonse.
Pano ndinabwerera kwa makolo anga ku mpoto kuti akambirane ndi mayi ake kuti mwina ndibwererenso ku banja kwanga. Iye akulimbikira kuti sakundifunanso.
Ndithandizeni Anatchereza kuti ndipange bwanji?
SK,
Mzimba
Moni moni SK,
Pamalo pena paliponse ngati ukukhalapo umayenera kukhala ndi mtendere. Ndiye ngati mtendere palibe, pamalo pamenepo sungakhalepo. Iwetu anthu amenewo sakukufuna. Ngakhale ungapange zabwino zotani koma anthu amenewo sakukufuna.
Mwamuna wakoyonso naye sakukufuna. Anakakhala kuti amakukonda bwenzi akumawakonza makolo ake zomwe akuchitazo.
Usakakamire banja lopanda chikondi. Banja limakhala bwino nonse mukamakondana. Chikondi ndi maziko a zonse. Ngakhale mwamuna akhale opanda ndalama koma ngati chikondi chilipo chachikulu mumakhala osangalala chifukwa zonse mukupangira limodzi.
Ngakhalenso umayesetsa kuwasangalatsa apongozi ako, iwo alibe nawe chikondi.
Limba mtima ndi kumuiwala mwamuna ameneyo.
Tili pa chibwenzi, ndizithandiza makolo ake?
Zikomo Anatchereza,
Ndine mnyamata wa zaka 28, ndili ndi chibwenzi chomwe chimagwira ntchito. Ine ndili pa ntchito. Chibwenzi changachi chandiuza kuti ndiyenera kumamuchitira chilichonse.
Akuti, kuti mkazi adziwe kuti mwamunayu adzamukwatira, mwamuna amayenera kumuchitila chilichonse, makolo akenso ndiziwathandiza kuti adziwedi kuti mwamunayu azamukwatira.
Anache kodi zimenezi ndi zoona? Komanso zimayenela kukhala choncho? Ine ndayamba kukaika.
Ndithandizeni ngati zili zoona.
Blantyre.
Zikomo a ku Blantyre,
Sizoona zimenezo. Akungofuna kukubera ameneyo. Pamene pali chikondi suchita kulamula kwa mnzako kuti ukufuna chithandizo.
Ngati mukukondana kwambiri. Zokha zimachita kuonetsa kuti anthuwa akwatirana. Zomwe akulamulazo zitha kupangitsa kuti usadzamukwatire mkaziyo.
Ngati zomwe walamulazo makolo ake akugwirizana nazo dziwa kuti anthu amenewo ndi ovuta kumanga nawo banja. Akungofuna ndalama zako osati chikondi.
Nanga ntchito itati yakuthera ameneyo adzakukonda? Chikondi sichimayenda choncho. Khala naye tcheru mkazi ameneyo.
Anatchereza.