Nkhani

Akuti mtima mmalo, chitetezo chilipo pa zisangalalo

Listen to this article

Nduna ya za chitetezo cha m’dziko a Ken Zikhale Ng’oma ati unduna wawo wakhwimitsa chitetezo m’nyengo ya zisangalalo za Khrisimasi ndi Nyuwere kuti Amalawi asangalale mwaufulu.

Koma kadaulo pa za chuma a Milward Tobias achenjeza kuti ponyadira chisangalalocho, makolo asaiwale kuti mwezi wa January 2024 afunika kupereka mafizi komanso kuyendetsa za kumunda.

Sitolo zazikulu zidali mbeee! kusiyana ndi mmbuyomu

Iwo anena izi potengera momwe chuma chikuyendera m’dziko muno potsatira kugwa kwa ndalama ya Kwacha komwe kwakweza mitengo ya zinthu.

Dziko lapansi makamaka a Khristu akhala akukondwelera Khrisimasi ndi chaka chatsopano (Nyuwere) kuyambira pa 24 December 2023 mpaka pa 2 January 2024.

Panyengoyi kumakhala maphwando komanso kugula zovala ndi mphatso zosiyanasiyana zomwe zimatenga ndalama zochuluka makamaka potengeranso kuti anthu amalandira malipiro awo msanga.

A Tobias omwenso akufuna kudzaimira pa mpando wa Pulezidenti m’chaka cha 2025 ati zisangalalo ngati izi zimapangitsa kuti pofika mmwezi wa January anthu ambiri akhale alibe ndalama.

“Zimakhala zomvetsa chisoni kuona makolo akusowa pogwira, ena mpaka ana kumadikira kuti alandire malipiro a January kuti apite kusukulu, uku n’kulephera kukonzekera kwa kholo,” atero a Tobias.

Iwo ati makolo a nzeru amayenera kuika padera ndalama za fizi ndi kumunda n’kuona kuti zotsalazo angapange nazo bwanji kuti banja lisangalale uku akudziwa chochita mu January.

A Zikhale Ng’oma ati Amalawi akamapanga mapulogalamu awo azisangalalo azipanga mtima uli mmalo kuti chitetezo alinacho kuchokera ku unduna wawo.

“Ndimanena nthawi zambiri kuti boma ili lili ndi chidwi pankhani yachitetezo, pano ndikutsimikizira Amalawi kuti tiwapatsa chitetezo chokwanira m’nyengo ya zisangalalo ndipo yemwe akufuna kuyesa chitetezocho ayese,” atero a Ng’oma.

M’nyengo ngati iyi, umbava, umbanda ndi ngozi za mitundu yosiyanasiyana zimachuluka koma a Ng’oma ati undunawo wakhazikitsa ndondomeko zokhwima.

“Amalawi asadabwe akaona apolisi ali balalabalala m’madera mwawo sikuti akukawamanga ayi koma ndi njira imodzi yomwe takhazikitsa kuti paliponse pazipezeka apolisi.

“Kupatula apo, muona zipata za chipikisheni zongokhazikitsa mwadzidzidzi m’misewumu, apolisi a njinga zamoto, magalimoto ndi woyenda pansi akhala paliponse m’madera azisangalalo kuti ateteze anthu,” atero a Ng’oma.

Andunawo atinso kupatula kudalira apolisi, chitetezo chachikulu cha munthu chimakhala ndi mwini wakeyo moti anthu akuyenera kutsina khutu apolisi msanga akadabwa ndizochita za wina.

Atinso oyendetsa galimoto akuyenera kuonetsetsa kuti galimoto zawo n’zoyenera kuyenda pamsewu, atsatire malamulo a pamsewu komanso omwe akuchoka pakhomo kukasangalala kwina akwimitse chitetezo pakhomo pawo.

Iwo adati monga zaka zonse akunenanso kuti kuti pochoka pakhomo anthu asasiya popanda munthu ayi, osalengeza m’masamba a m’chezo kuti simuli pakhomo.

Malinga ndi a kulikulu la polisi ku Lilongwe, pakati pa 24 December 2022 ndi 2 January 2023, anthu 20 adamwalira pomwe ena 70 adavulala pangozi 56 zomwe zidachitika panyengoyo.

Pokonzekera chitetezocho, apolisi m’maboma ena ayamba kale kusesa anthu ophwanya malamulo kuti panyengo ya zisangalalo anthu otero asasokoneze anzawo.

M’boma la Balaka, anthu 15 adagwidwa pachipikisheni cha pa 17 December 2018 pa milandu yosiyanasiyana monga kuthyola ndi kuba, kupezeka n’katundu obedwa, kugonana ndi ana, kuvulaza mnzawo ndi kupezeka malo osayenera kupezekapo nthawi yolakwika.

Mneneri wapolisi ya Mponela a Macpatson Msadala ati kumenekonso apolisi akhala akukumana ndi mafumu, anthu m’midzi, ochita malonda ndi adindo ena kukambirana nawo zachitetezo.

Related Articles

2 Comments

Back to top button
Translate »