Nkhani

Owaganizira kupha anthu 4 amangidwa

Listen to this article

Apolisi amanga anthu 6 omwe akuwaganizira kuti adatengera lamulo m’manja mwawo potengapo gawo pa kuphedwa kwa abambo 4 omwe amaganiziridwa kuti amakaba m’boma la Thyolo.

Wachiwiri kwa mneneri wapolisi m’dziko muno a Alfred Chimthere ati anthuwo amangidwa potsatira kafukufuku wa apolisi atalandira lipoti loti abambo 4 adaphedwa pa 19 December 2023 kwa Njema mfumu yaikulu Mabuka ku Thyolo.

“Anthuwo tawamanga chifukwa adaphwanya lamulo, timanena nthawi ndi nthawi kuti tikagwira munthu oganiziridwa mlandu tizipita naye kupolisi chifukwa amakhala othandiza pa kafukufuku,” atero a Chimthere.

Iwo ati kupatula kuphwanya lamulo, kupha oganiziridwa mlandu ndi kuphwanya ufulu wa munthu okhala ndi moyo komanso zimanyozetsa ulemu wa umunthu wa chilengedwe.

Nkhani ikuti abambo 4 adapezeka akukaba ku golosale ya wa bizinesi wina ku misewu folo m’mudzi mwa Njema kwa mfumu yaikulu Mabuka ku Thyolo ndipo awiri adagwidwa pomwe ena awiri adathawa.

Nkhaniyo ikupitiriranso kuti awiri omwe adagwidwawo adaulula anzawo asadaphedwe ndipo kenako anthuwo adanka nasaka awiri enawo omwe atawagwira adawaphanso.

Abambo omwe adaphedwawo onse amachokera m’mudzi mwa Chipwaila mfumu yaikulu Chikumbu koyandikana ndi komwe amawaganizira kuti amafuna kukabako.

A Chimthere ati anthu omwe agwidwa poganiziridwa kutenga gawo pa kuphedwa kwa abambowo ndi a Gift Manuel a zaka 37, a Nedson Taulo azaka 50, a Shadrec Manuel a zaka 52, a Thokozani Semion a zaka 26, a Billy Yamikani a zaka 30 komanso a John Malichi a zaka 32.

Iwo ati anthu onsewa amachokera m’mudzi mwa Mtiza kwa mfumu yaikulu Mabuka ku Mulanje ndipo akayankha mlandu wakupha kubwalo la milandu posachedwapa.

Abambo omwe adaphedwawo ndi a Willy Manyowa omwe zaka zawo sizikudziwika koma ndi achikulire, a John Maudzu a zaka 31, a Madalitso Mailosi a zaka 25 pomwe winayo sakudziwika.

A Chimthere ati m’nyengo ya zisangalalo yomwe yafikayi oganiziridwa milandu amakhala ochuluka ndipo apempha anthu kuti akagwira munthu oganiziridwa azipita naye kupolisi kuti apolisi apange kafukufuku wawo nkuyendetsa nkhaniyo motsata malamulo.

Related Articles

Back to top button
Translate »