Alimi otsogola amasamalira nthaka

 

Chuma chili mu nthaka, komatu sichipezeka mu nthaka yosakazidwa. Kusasamala za chilengedwe monga mitengo kukupangitsa kuti nthaka iziguga. Izitu zikusautsa alimi chaka chilichonse potaya nthawi ndi ndalama zawo m’minda yokanika kupereka zipatso zoyenera. Ngakhale zili chonchi, alimi ena akusimba lokoma chifukwa minda yawo ili ndi mphamvu zogonera. M’modzi mwa alimiwa ndi Joseph Khoswe wa m’mudzi mwa Matipa mu Chingale EPA m’boma la Zomba yemwe akubwekera dongosolo losamala nthaka ndi akalozera. TEMWA MHONE adacheza ndi Khoswe motere:

Alimi ena mu Chingale EPA ku Zomba kuunga mlambala pansi pa chingwe cha kalozera

Panopa tiziti kwacha moti alimi azipita ku munda?

Eya. Ulimitu ulibe tchuthi. Kudacha kalekale titakolola mu April. August ndi mwezi wogalauza apo ndi apo. Lingaliro lokonza minda mvula ikayamba kapena masabata awiri isadagwe likuchititsa ulimi m’dziko muno kukhala wovuta. Chizolowezichi chimayipitsa mbiri ya ulimi pomaganiza kuti ulimi ndi magobo chifukwa timachita zinthu zambiri mu nthawi yochepa pothamangitsana ndi mvula.

Mukuukokomezatu ulimi mpaka levulo ku munda?

(Akuseka) Pomwe pali chuma palibe kusewera. Ulimi ndi bizinezi yodalira nthaka yomwe timayenera kuyisamala chaka chonse. Pambali pa mavuto odza ndi kusintha kwa nyengo, mugwirizana nane kuti ambiri ulimi ukuwakanika chifukwa minda idaguga ndipo mbewu sizikubereka moyenera. Levuloyi (yogwiritsa ntchito amisili omanga nyumba poyala njerwa) ndi chimodzi mwa zida zokonzera akalozera oteteza nthaka. Zina ndi zikhomo, chikwanje, chingwe cha mamita 5, mitengo (ndodo) iwiri yotalika mamita 1.6 mpaka 2.0 ndi hamala.

Akalozera ndi chani?

Ndi dongosolo lopezera kayendedwe ka madzi m’munda ndi cholinga chokonza mizere yoteteza nthaka. Mwachitidwa akalozera  timaungamo milambala yomwe imateteza nthaka pochepetsa kuthamanga kwa madzi m’munda. Mizere yonse yotsatira imalunjika mlambalawo. Potengera kutsika kwa malo, akalozera kapena milambala imene imatalikana 5 kapena 10 mitazi m’munda.

Mumakonza motani akalozera?

Timafunika anthu atatu. Awiri aima ndi ndodo zomangidwa chigwe chija ndipo ine ndikhala pakati ndi levuloyi kuyeza. Malo omwe timadzi mu levulo tabwera pakatikati wa kumapeto amaika chikhomo ndi kusunthira komwe kuli ndime. Timatero mpaka munda wonse uthe.

Dongosololi ndi lofunika bwanji m’munda?

Kuteteza nthakako ndiye kuti chonde sichikokoloka, komanso amathandiza chinyezi kukhalitsa m’munda polowetsa madzi okololedwawo pansi. Ndi yankho ku vuto la ng’amba ndi kuguga kwa nthaka monga madongosolo ena ophimbira, ngonyeka (box ridges), ulimi wa m’maenje ndi maswale.

Mwapindula motani ndi akalozera?

Chajira kaya muti chonde m’munda mwanga ndi chogonera. Kukagwa ng’amba, ndi maonera kufoota kwa mbewu za alimi ochita chisawawa poti mwanga chinyezi chimakhalitsanso. Zokolola ndi kholophethe mpaka ndidasankhidwa kukhala mlimi wachitsanzo kumbali ya akalozerayi.

Mawu kwa anzanu?

N’zotheka kupindula ndi ulimi pakati pa mavuto odza ndi kusintha kwa nyengo. Mbewu kuti zichite bwino zimafuna chonde ndi madzi zomwe zimatetezeka ndi akalozerawa.  Tizikonza mwachangu minda kuti tikhale gulu la ochepa ongomva kuti zokolola zikuchepa masiku ano. n

 

Share This Post

Powered by