Amayi ayiphula ndi a Mpinganjira
Lachinayi sabata yatha lidayamba monga tsiku ngati lililonse kwa mayi Mary Chikaonda omwe amaotcha tchipisi komanso zipalasilo ndi mitu ya nkhuku pa msika wa Njuli ku Chiradzulu.
Monga mwa chizolowezi, iwo adalawirira kupita pa malo awo a bizinesi ndipo pomwe nthawi imakwana 8 koloko, adali atayambapo.
Koma iwo samayembekezera kuti chozizwa chitha kuwachitikira mkati mwa tsikulo.
“Ndinadekha monga mwa masiku onse kuchita bizinesi ndi pamene ndinaona gulu la anthu likuyendayenda pa msika pano,” iwo adatero.
Iwo sadatutumuke popeza adazolowera kuti pa msika pamapita anthu osiyanasiyana ndi zolinga zawo. Pamenepa ndi kuti nthawi ili m’ma 11 koloko m’mawa.
Posakhalitsa, anthu omwe adafika pa msikapo adayandikira pa malo awo a bizinesi.
Apa ndi pomwe adadabwa chifukwa khwimbilo limatsatira mayi Triephornia Mpinganjira omwe amachita mabizinesi osiyanasiyana.
“Atafika pa bizinesi yanga anati akufuna kugula tchipisi ndipo ndidawapatsa cholawa kaye. Kenako tidayamba kucheza pomwe amandifunsa za bizinesi komanso mavuto omwe ndikukumana nawo,” adatero a Chikaonda.
Atamaliza kucheza, a Mpinganjira adawauza kuti akufuna kuwathandiza powapatsa K500 000 yoti aonjezere mpamba wa bizinesi.
Izi zidadzetsa chimwemwe kwa a Chikaonda omwe adakuwa ndi kukhetsa msozi chifukwa cha msangala.
“Kutereko bizinesi siyikuyenda zomwe zikundisokonezanso ku nyumba. Koma apa ndalamayi indithandiza zedi,” iwo adatero.
Ndipo pomwe a Mpinganjira amapita pa malo ena, a Chikaonda adali akuimba nyimbo zotama Mulungu komanso kuthokoza uku akuvina.
Ena omwe adalandira ndalamazi pa msika wa Bvumbwe, mayi Alice Wonderful, sadabise chimwemwe chawo.
“Apa ndipezanso bizinesi ina kupatula yogulitsa masambayi popeza sizikuyenda. Kubwera kwa a Mpinganjira ndi mdalitso waukulu,” adatero iwo.
Ndipo pomwe a Mpinganjira amachoka pa malo a Wonderful kupita pena, iwo adali akuyalula masamba awo kuweruka kuopetsa kuti achitidwa chipongwe.
Tsikulo a Mpinganjira adapereka ndalama kwa amayi 10 pa misika ya Njuli ku Chiradzulu ndi Bvumbwe ku Thyolo. Iwo adapereka ndalamazo pofuna kutukula amayi a kumudzi ochita malonda ang’onoang’ono.
Iwo aika padera ndalama zokwana K20 miliyoni zoti apereke kwa amayi a ku mudzi ochita mabizinesi m’dziko lino.
Poyankhula atamaliza kupereka ndalamazi, a Mpinganjira anati iwo akufuna kuthandiza amayi ochita malonda m’madera a ku mudzi.
“Komanso ndikufuna kuwalimbikitsa amayi anzanga kuti ngati bizinesi siyikuyenda, achilimike popeza pena zimakhala choncho. Koma pa zonse, thandizo limafunika, n’chifukwa ndabwera kupereka ndalamazi,” adatero a Mpinganjira.
Iwo anati khumbo lawo ndi lofuna kutukula amayi komanso kuwapatsa upangiri kuti akwanitse kukhala odziimira paokha.
Malingana ndi a Mpinganjira, miyezi ikubwerayi ayamba kupereka ndalama zokwana K1 miliyoni kwa achinyama kuti azikwanitsa kuzithandizika pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku.