Anjata opezeka ndi mfuti
Apolisi ku Namwera m’boma la Mangochi amanga abambo awiri omwe angotulutsidwa kumene kundende popezeka ndi mfuti ya mtundu wa Retay Pistol ndi zipolopolo ziwiri.
Mneneri wa polisi ya Mangochi mayi Amina Tepani Daudi wati amunawa ndi a Bashir Ayami a zaka 20 ndi a Mustapha Antonio Stanley a zaka 34 omwe omwe amachokera kwa Mfumu Yayikulu Jalasi m’bomalo. Apolisiwo adagwira awiriwo pa 5 June 2024 pamsika wa Namwera.
“A Ayami akhala akuthawathawa pambuyo pothawa kundende ya Mangochi mu March chaka chino pomwe a Stanley anagwirapo ukaidi pa mlandu wakuba mwa upandu,” adatero iwo.
A Daudi anati patsikulo apolisi adatsinidwa khutu ndi anthu akufuna kwabwino kuti awiriwa akusunga mfutiyo ku Namwerako.
Adaonjeza matekitivi apolisi adathamangira kumaloko komwe adagwira awiriwo ndi kupezanso mfuti ya pistol ndi zipolopolo ziwiri.
A Daudi adati kuonjezera apo a Stanley adawapeza ndi njinga yakapalasa yomwe iwo anaulula kuti anayiba ku Nsanama m’boma la Machinga.
Atafunsidwa a Ayami adati atathawa kundende adapita m’dziko la South Africa komwe adakagwirizana ndi a Stanley ndi akuba ena kuti abwere kumudzi pambuyo pa kuba pistol.
A Daudi anati pakalipano a Ayami awatsegulira milandu yothawa kundende komanso yopezeka ndi mfuti wopanda chilolezo pomwe a Stanley awatsegulira milandu yopezeka ndi mfuti popanda chilolezo komanso wakuba.
Izi zili apo, bwalo la Chikwawa First Grade Magistrate, Lachisanu latumiza abambo enanso awiri kundende atawapeza wolakwa pamlandu woba abulu.
Bwalolo, kupyolera mwa wapolisi woimira boma pa milandu a Danford Otala, lidamva kuti awiriwa, Steven Bira a zaka 26 ndi a Doloben Maxwell a zaka 25 pa 27 May 2024 adaba abulu anayi a mlimi wina wa m’mudzi wa Chigwata omwe ndalama zake ndi zokwana K2 miiyoni.
Ataonekera pabwalo la mlandu, awiriwa adavomera mlanduwo. Uku n’kuphwanya gawo 281 la malamulo woyendetsera milandu ya upandu m’dziko lino.
Popereka madandaulo awo, awiriwo anaseketsa anthu popempha belo ponena kuti anapezeka kale wolakwa ndi kulamulidwa.
Koma a Otala adapempha chilango cha mkati ponena kuti abulu amagwiritsidwa ntchito pa nkhani ya mtengatenga ndi maulendo kumudzi.
Naye woweruza Joram Zebron adagwirizana ndi woimira boma ndipo adalamula kuti Bira ndi Maxwell akagwire ukaidi wa kalavula gaga kwa zaka zitatu kuti likhale phunziro kwa andipsi ena.
A Bira amachokera kwa Jana pomwe a Maxwell kwawo ndi kwa Muyambusa Mfumu Yayikulu Chapananga m’boma la Chikwawa.