Nkhani

 Anyumwa ndi zitupa za unzika m’nkhokwe

Kudali mpungwepungwe Lachitatu pomwe aphungu a mbali yotsutsa boma adakapeza zitupa za unzika ku nkhokwe yosungirako chimanga ya National Food Reserve Agency (NRB) ku Kanengo mu mzinda wa Lilongwe.

Mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma a George Chaponda adauza Nyumba ya Malamulo kuti aphunguwo ankafuna kukaona kuchuluka kwa chimanga ku nkhokweko koma adadodoma kuti mudadzadza ndi zikwizikwi za zitupa.

Zipangizo zimene a NRB amagwiritsa ntchito ku nkhokwe | Nation

A Chaponda adati aphunguwo s adamvet se kut i z i tupazo zidakapezeka bwanji ku nkhokweko ndipo adaweruza kuti ndiye kuti chipani cha MCP chimafuna kudzabera chisankho pogwiritsa ntchito zitupazo.

“Takhala tikunena kuti a MCP ali ndi pulani yodzabera chisankho, APA zaoneka zokha. Ulendo wokaona chimanga takapezako zitupa za unzika zili milu milu m’nkhokwe ya chimanga. Amatibisira chiyani otsutsafe?” adatero a Chaponda.

Koma mtsogoleri wa Nyumba  ya Malamulo a Richard Chimwendo Banda adati otsutsa angodzadzidwa ndi mantha kuti sangadzapambane chisankho ndiye kalikonse kangachit ike ndi boma likufuna kudzabera.

“Nthambi ya kalembera wa unzika ya NRB yafotokoza kale momveka bwino momwe zitupazo zidakapezekera kumene zidal iko ndipo kuti chimachitika n’chiyani tsono anzathuwo adangoona n’kuyamba kufalitsa bodza osafunsa kaye,” adatero a Chimwendo Banda.

Iwo adatsimikiza kuti pa l ibe chomwe boma likupanga chosonyeza kufuna kudzabera zisankho ndipo ati anthu akamva kapena kuona kalikonse kokaikitsa aziyamba afunsa asadafalitse bodza.

Polongosola za momwe zitupazo zidakapezekera ku nkhokweyo, mlembi wamkulu wa bungwe la NRB a Mphatso Sambo adati nthambiyo ima f una ma l o aa ku l u ounikirako zitupa kuti zizipita koyenera.

Iwo adati bungwe la UNDP lomwe limathandiza kwambiri pa zisankho ndilo lidalipira malowo komanso za mtundu omwewo zimachitika ku Mmwera ndi ku Mpoto.

“Tikungogwira ntchito y a t h u s i k u t i n s o t i l i kumbuyo kwa chipani chili chonse ayi. M’nyumba imeneyi m’mafikira zitupa zosiyanasiyana zikapangidwa ndi ye timaf unika malo wotakasuka woti ziziunikidwa n’kuona kuti zikuyenera kukaperekedwa,” adatero a Sambo.

Nkhaniyo itaphulitsidwa ndi aphungu otsutsa boma, NRB idaitanitsa atolankhani, oyimilira UNDP, a mabungwe komanso oimirira zipani za ndale kuti akawafotokozere chilungamo cha zomwe zimachitika.

Mkulu wa NFRA a George Macheka adatsimikiza kuti a UNDP komanso bungwe loona za zakudya pa dziko l o nse la WFP ndiwo amachita lendi malowo koma sakudziwapo kanthu za a NRB.

“Amachi ta lendi ndi mabungwe awiriwo omwe amathandiza NRB pa zina ndi zina. Palibe mgwirizano ulionse ndi a NRB,” adatero iwo.

Koma mlembi wamkulu wa chipani cha DPP a Peter Mukhito adati ngosakhutira ndi yankho lomwe a Sambo adapereka ngakhale kuti iwo komanso mtsogoleri wa chipani cha Aford a Chakufwa Chihana adali nawo kokaona zitupazo.

Lachitatu, zokambirana m’Nyumba ya Malamulo zidathera panjira kaamba ka kusemphana pakati pa mbali ya boma ndi mbali yotsutsa boma pa nkhani yomweyi.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Check Also
Close
Back to top button