Nkhani

Apempha kafukufuku pa CDF

Pomwe chiwerengero cha anthu maka abambo odzipha chikupitirira kukwera m’dziko nacho chiwerengero cha achinyamata makamaka omwe ali sukulu za ukachenjede chikukwera.

Mwa zina mavuto a za chuma ndi omwe nthawi zambiri akukhala akuyambitsa mavutowa malinga ndi akatswiri pa nkhani za maphunziro.

Ophunzira alandire upangiri. I Nation

Thumba  la CDF muli K200 miliyoni ndipo gawo lina limayenera kupita ku ntchito yopereka fizi kwa ana anzeru koma osauka kuti alipire sukulu. Koma nthawi zambiri ndalamayi siioneka.

Mmodzi mwa akatswiriwa a Benedicto Kondowe ati pakufunika kuti pakhale kuunikanso bwino mmene ndalama yomwe imaikidwa kuti ithandizire kumbali ya maphunziro pansi pa ndondmomeko ya CDF  ikugwirira ntchito.

Iwo ati ndi zomvetsa chisoni komanso zopereka chiopsezo makamaka pa nkhani yokhudza tsogolo la dziko lino ponena kuti likuluza achinyamata omwe akadatha kulichotsa dziko lino pa mavuto omwe likudutsamo.

A Kondowe adati: “Monga mukudziwa, chomwe chimayambitsa vuto la kudzipha nthawi zambiri ndi vuto la malingaliro a ngwiro omwe amasowa pakakhala mavuto a za chuma.

“Pakufunika kuika poyera ndondomeko zofotokozera momwe ndalama ya CDF imagwirira ntchito pofuna kuti anthu azitha kutsata komanso kudziwa momwe ndalamayi ikugwirira ntchito,” adatero iwo.

Iwo adatinso pakufunika kuti sukulu zilembe akatswiri a za kaganizidwe kabwino kuti azipereka upangiri kwa ophunzira ndipo aonjeza kuti boma lizilimbikitsa mabungwe omwe amagwira ntchito yopereka malangizo pa za kaganizidwe kabwino kuti azitha kugwira ntchito zawo m’sukulu.

“Pakufunikanso kuti anthu m’madera azitenga mbali pothandiza ophunzira komanso kuti m’sukulu zathu mukhala magulu omwe ophunzira azitha kukumana ndi kugawana nkhawa zawo pofuna kupeza thandizo,” adatero iwo.

Mmodzi mwa akadaulo pa za maphunziro a Lexon Ndalama adagwirizana ndi a Kondowe ponena kuti mavuto a za chuma komanso kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo ndi ena mwa mavuto omwe akukolezera mchitidwewu.

“Sukulu za ukachenjede zili ndi thumba limene limathandiza ophunzira omwe alibe kuthekera komanso boma lili ndi thumba lomwe limabwereketsa ndalama kwa ophunzira la The High Education Loan Scheme. Koma pakufunika kuika chidwi poonetsetsa kuti omwe akupindula ndi thumbali ndi woyenera kutero pofuna kuthana ndi mavuto odzipha,” adatero iwo.

Koma mneneri mu unduna wa za maphunziro m’sukulu za ukachenjede a Gift Chiponde adati undunawu udakhazikitsa nthambi zoti zizithana ndi mavuto omwe ophunzira akukumana nawo.

“Unduna wa maphunziro aukachenjede udapereka mphamvu kwa sukulu zonse kuti zilembe ntchito akatswiri pa nkhani za kaganizidwe ka ngwiro omwe amatchedwa kuti psycho-social counsellors m’Chingerezi kuti azitha kuthandiza ophunzira,” adatero iwo.

Iwo adati undunawu umalimbikitsanso bungwe lopereka ngongole kwa ophunziralo kuti liziphunzitsa aphunzitsi momwe angathandizire ophunzira akakumana ndi mavuto komanso kuwathandiza pa maluso osiyanasiyana.

Titafunsa mneneri wapolisi mdziko muno a Peter Kalaya kuti ayikepo mlomo adati sangathe kulankhula pa nkhaniyi.

“Ndili ndi matha, sindingathe kufotokoza za chiwerengero cha ophunzira omwe amadzipha kaamba koti pa kagwiridwe kathu ka ntchito sitikhala ndi chiwerengero chapadera chokhudza ophunzira pa nkhani zodzipha,” adatero iwo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Check Also
Close
Back to top button