6 July ili ku BNS
Nduna ya zofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu apempha Amalawi amene akudzapita ku chisangalalo choti dziko lino lakwanitsa zaka 61 lili pa ufulu wodzilamulira kuti adzapewe kutenga zakumwa zoledzeretsa ngakhalenso kunyamula zida popita ku mwambowu ku Bingu National Stadium (BNS) mawa.
Pa 6 July chaka chilichonse, kumakhala mwambowu ndipo Kunkuyu ati mutu wachikondwelero cha chaka chino ndi kumanganso maziko oweyeseka.

A Kunkuyu ati mwambowo uyamba lero Loweruka ndi mapemphero ndipo udzapitirira mawa ndi zochitika zosiyanasiyana monga masewero a pakati pa timu ya Flames ndi Botswana komanso magule a makolo athu.
“Uwu ndi mwambo omwe umayenera kutikumbutsa umodzi wathu. Tsiku limeneli tonse timayenera kuiwala kusemphana kwathu pa ndale kapena zipembedzo chifukwa ndi tsiku lomwe timakondwera kuti tidapeza ufulu wodzilamulira,” atero a Kunkuyu.
Iwo apempha Amalawi kuti adzapewe kutenga zakumwa za ukali komanso zida popita ku mwambowo ndipo ana sadzaloledwa kulowa ku BNS okha popanda makolo awo.
“Izi tachita chifukwa tikufuna kuti kusadzakhale chisokonezo kapena mavuto ena ndi ena. Kudzakhala chitetezo chokhwima ndipo polowa pakhomo padzakhala opanga chipikisheni,” atero a Kunkuyu.
M’chaka cha 2017, anthu asanu ndi atatu 8 adamwalira komanso ena ambiri adavulala kutsatira chisokonezo chomwe chidabuka ku bwalo lomwelo pa tsiku la chisangalalo ngati chomwechi.
Malingana ndi a Kunkuyu, n’chifukwa chake boma lakhwimitsa chitetezo pa chikondwererocho kufuna kuteteza nzika ndi alendo omwe adzakhale nawo pa mwambowo.
Mlendo wamkulu yemwe watsimikizika kuti adzakhale nawo pa mwambowo ndi pulezidenti wa dziko la Botswana a Duma Gideon Boko omwe akuyembekezeka kufika mdziko muno lero kudzera kubwalo la denge la Kamuzu International Airport (KIA).
Lero kummawa kuno, atsogoleri amipingo yosiyanasiyana atsogolera mapemphero ku BNS kukonzekera mwambo weniweni mawa pomwe kudzakhale zolankhula zosiyanasiyana.
Womenyera ufulu anthu a Michael Kaiyatsa ati uwu ndi mpata woti atsogoleri akhoza kugwiritsa ntchito polalikira za mtendere ndi umodzi pano pomwe mitima ya anthu idakwera kale kaamba ka nkhani ya zisankho zomwe zikudza pa 16 September 2025.
“Tsikuli lili ndi tanthauzo lalikulu moto mpofunika kuligwiritsa ntchito bwino. Zakhala bwino kuti boma latsogoza kale za mtendele ndipo akuyenera kudzalalika zomwezo pa mwambowu,” atero a Kaiyatsa.