Apempha MEC iyalule mphasa

Bungwe la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) lati potsatira chigamulo cha khoti kuti bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) silidayendetse bwino chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino, wapampando wake Jane Ansah ndi makomishona onse atule pansi udindo mwaulemu.

Foni yake idaduka: Ansah

Wapampando wagululo, Timothy Mtambo, wati momwe chigamulochi chakhalira, bungwe lawo latenga mangolomera apadera ndipo ayesetsa mpaka aone kuti Ansah watula pansi udindo.

HRDC yakhala ikutsogolera zionetsero zofuna kuchotsa Ansah pampando polingalira kuti sadayendetse bwino chisankho cha pa 21 May 2019 koma polankhula ndi wailesi ya Zodiak Broadcasting Station (ZBS) mmbuyomo, Ansah adati adzatula pansi udindo khoti likadzamupeza olakwa.

“Zachitika, khoti latimasula kuti chisankho sichidayende bwino chifukwa cha MEC ndiye tikudikira kutula pansi maudindo a makomishona ndi Ansah ku MEC uko apo ayi tichita kuwachotsa,” watero Mtambo.

Mwa zifukwa zina popereka chigamulo, khoti lidapeza kuti makomishona a MEC adavulira mphamvu zawo mkulu woyendetsa zisankho Sam Alfandika motsutsana ndi malamulo ndipo pachifukwachi, zambiri zidayenda chidule komanso mosokonekera.

Potanthauzira zomwe chigamulochi chikunena, katswiri pa malamulo Henry Chingaipe wati kutengeradi chigamulocho, Ansah ndi makomishona anzake akuyeneradi kuchoka ku MEC koma wati pali njira ziwiri.

“Malamulo a dziko amapereka mphamvu zosankha kapena kuchotsa makomishona onse kuphatikizapo wapampando wake, koma malamulo omwewo amapereka mphamvu ku komiti ya zosankha maudindo ku Nyumba ya Malamulo kuti ikhoza kuunguza MEC kapena komishona ndipo ngati akulephera ntchito, komitiyo ilembele kalata Pulezidenti kuti achotse wolepherayo.

“Tsono momwe zilili apapa, komiti siyikuyeneranso kuunguza ayi koma kungotenga zomwe khoti lidanena n’kulemba kalatayo basi. Apo ayi, njira ina, Ansah ndi makomishona anzake pawokha angotula pansi maudindo mwaulemu,” watero Chingaipe.

Katswiri pa kayendetsedwe ka zinthu m’dziko Makhumbo Munthali naye wati ndi momwe chigamulo chidabwerera, MEC ilibe kothawira koter makomishona ndi Ansah akuyenera kutula pansi maudindo awo.

“Umboni udaperekedwa m’khoti uja ndi wamphamvu moti zangovuta kuti n’kuno kwathu anthu amakakamira maudindo koma kukadakhala maiko ena akunja, mukadamva kale lomwe lija kuti anthu atula pansi maudindo,” adatero Munthali.

Pomwe kadaulo pandale George Phiri wati sakutha kumvetsa chomwe Ansah ndi akuluakulu ena akufuna kubisa pokakamira m’mipando yomwe ngakhale eni ake akudziwa kuti akuyenera kuchokamo.

“Sikuti sakudziwatu, enawo ndi a zamalamulo ndiye tanthauzo la zomwe zikuchitika akulidziwa bwino lomwe koma, pakukaikitsa mpoti kodi chikuwakanikitsa kutula pansi udindo n’chiyani, kapena pali chomwe akuteteza,” watero Phiri.

Titamuyimbira lamya Ansah kuti timve mbali yake, iye adangodula lamyayo atamva funso ndipo sitidapitirize kumuimbira.

Share This Post

Powered by