Nkhani

Aphungu akumana Lolemba

Pamene aphungu ayambe kukumana Lolemba posanthula ndondomeko ya pakati pa chaka ya momwe boma lagwiritsira ntchito chuma, sipikala wa Nyumba ya Malamulo Catherine Gotani Hara wati aphungu akambirananso nkhani zimene bwalo la milandu idati aunikire sabata yachiwiri.

Iye adati nyumbayo igwira ntchito usana ndi usiku poyesetsa kuika malamulo okwaniritsa zomwe bwalo la milandu lidalamula Lolemba.

Gotani Hara: Aphungu sachitanso kufunsa mafunso

Popereka chigamulo chawo Lolemba, pomwe oweruza adati chisankho cha pa 21 May sichidayende mwa chilungamo ndipo adalamula kuti chisankho chichitike pakutha kwa masiku 150, bwalolo lidapereka mphamvu ku Nyumba ya Malamulo kuti ikonze ndondomeko zina kuti chisankhocho chidzachitike mosavuta.

Mwa zina bwalolo lidalangiza aphungu kuti akalongosole za gawo la malamulo limene limanenetsa kuti wopambana pachisankho azipeza mavoti oposa 50 mwa 100 alionse.

Polankhula pamsonkhano wa atolankhani Lachinayi mumzinda wa Lilongwe, Hara adati aphunguwa akambirana za lamulolo sabata yachiwiri ya zokambirana zawo zomwe ziyambe Lolemba likudzali.

“Nyumbayi siyifunsanso maganizo pa nkhaniyi kwa anthu ena ambiri okhudzidwa koma kwa mkulu wa za malamulo m’boma yekha chifukwa ndi lamulo lochokera kubwalo la milandu,” adatero iye.

Hara adatsutsa zomwe anthu ena akhala akunena zoti nthambi yoweruza milandu idalowelera ku nthambi yopanga malamulo yomwe ndi Nyumba ya Malamulo.

“Palibe chomwe abwalo adalakwitsa iwo adagwira ntchito yawo yotanthauzira malamulo ndipo adangotithandiza kumvetsa bwino zomwe lamulo amanena. Kuchokera apo atipatsiranso nafe kuti tikhazikitse lamulo ndi ndondomeko zoyenera mmasiku 21,” adalongosola.

Iye adati koma zonse zikhonza kusintha ngati angalandirenso lamulo lina kuchokera kukhoti monga kuimitsa chigamulo cha Lolembacho.

Pogwirizana ndi Hara, kadaulo wa za malamulo pasukulu ya ukachenjede ya Chancellor Colllege wati izi zikutanthauza kuti tsopano dziko lino lizitsata lamulo la 50+1 posankha mtsogoleri.

Sunduzwayo Madise adati oweruza milanduwa adangotanthauzira lamulo la chisankho m’dziko muno kuti opambana azikhala wasankhidwa ndi anthu 51 pa 100 aliwonse osati kuchepera apo ndipo sadapange kapena kusintha lamulo lililonse.

Iye adati oweruzawo, Lolembali adatanthauzira lamulo la chisankho

mosiyana ndi momwe lidatanthauzidwira m’chaka cha 1999, pa mlandu omwe Gwanda Chakuamba adasumira bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission(MEC).

Malingana ndi Madise, omwe amaweruza mlanduwo, adaunikira ndi kupeza kuti pa mlandu wa Chakuamba wa 1999, lamulo lidatanthauzidwira molakwika ponena kuti wopambana ngati mtsogoleri wa dziko lino ndi yemwe wangotsogola basi ngakhale atasankhidwa ndi anthu ochepera 51 pa 100 aliwonse.

“Oweruza mlandu sikuti asintha lamulo lililonse, ayi. Iwowa angotathauzira mawu omwe m’Chingerezi timati majority kapena kuti ochuluka pa Chichewa. Iwowa atanthauzira kuti malinga ndi malamulo oyendetsera zisankho a dziko lino ochuluka akutathauza kusankhidwa ndi anthu osachepera 51 pa 100 aliwonse,” adalongosola motero.

Madise adati  lamulo la 50+1 lakhala lilipo m’malamulo a dziko lino nthawi yonseyi ndipo mmbuyomu takhala tikulakwitsa.

“Apapa ilili ndi lamulo ndithu basi, Nyumba ya Malamulo ingoika ndondomeko zake, zoyendetsera chifukwa tikabwerera mmbuyo, nthawi ya Chakuamba, palibe adapitanso ku nyumbayi kukafunsa, chigamulo chitaperekedwa, dziko lidangotsatira zomwe a khoti adanena,” adalongosola motero.

Pofunsidwa kuti bwanji a malamulo sankalowelera mmbuyo monsemu koma kumangoonerera zinthu zikulakwika, iye adati bwalo la milandu limadikira wina alipangitse kuchita zinthu ndipo silichita zinthu palokha ayi.

Iye adati apapa zatsala kwa Nyumba ya Malamulo kuti ikumane ndi kuika ndondomeko zoyenera monga momwe angayendetsere zisankho kutapezeka kuti palibe yemwe wapeza mavoti 51 pa 100 aliwonse mwina popikisana anthu anayi, mwachitsanzo.

Pomwe adaonjezeranso kuti Nyumba ya Malamuloyi ikuyenera kuikanso ndondomeko yoti zisankho zachibwereza pakakhala kuti sipadapezeke wopeza 50+1 zizichitika patadutsa masiku angati komanso kuti azipikisana ndi ndani.

Padakalipano mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika wati akasuma kubwalo lalikulu la milandu kuti chigamulocho sichidayeende bwino.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button