Nkhani

Aphana pachibale kaamba ka malo

Apolisi m’boma la Lilongwe amanga abambo atatu a banja limodzi powaganizira kuti adapha mbale wawo polimbirana malo m’mudzi mwa Maliseni kwa mfumu yaikulu Chadza.

Mneneri wapolisi m’boma la Lilongwe a Hastings Chigalu atsimikiza ndipo ati kupatula kupha a Moffat Kamunthu a zaka 39, abambo atatuwo akuzengedwanso mlandu wovulaza anthu ena ochokera kubanja la malemuyo.

“Anthuwo ndi a mabanja awiri koma pa chisuweni, ndiye amalimbirana malo koma kaamba kosamvana ngakhale mafumu adalowelerapo, adamenyana kwambiri pa 24 June 2023 pomwe malemuyo adafera pomwepo ndipo ena adavulazidwa,” atero a Chigalu.

Iwo ati nkhaniyo itafika povuta, idapita kubwalo la nyakwawa Nsabwe omwe adagamula mokomera banja la malemuyo koma siyidathere pompo chifukwa banja linalo lidatengera nkhaniyo ku mabwalo ena koma konseko nkhani imakomera banja la malemu.

Iwo ati chifukwa choonetsa kusakhutirabe, mafumuwo adawauza kuti akachite apiro ku bwalo la mfumu yaikulu Chadza.

“Nthawi ili m’ma 7 madzulo pa 24 June pomwepo oganiziridwawo adazingira mwana wochokera kubanja la malemu akuchoka ku msika ndiye poti abale ake akamulanditse ndewu ya zida idayamba.

“Mkatikati mwa ndewu, a banja linalo adakhapa a kubanja la malemu koma pomwe ena onse adakwanitsa kuthawa, malemuyo adaumbiliridwa mpaka kukomoledwa pomwepo n’kukafera ku chipatala cha Mitundu,” adalongosola choncho a Chigalu.

Abambo oganiziridwawo ndi a Marko Kambiya a zaka 41, a Innocent Kambiya a zaka 20 ndi a Bernard Kambiya a zaka 19 ndipo paomwe nkhaniyo imatipeza n’kuti apolisi akudikira zotsatira za chomwe chidapha malemuyo kuti atsegule milandu.

Pa 7 June 2023, apolisi ya Ntchisi nawo adamanga a Daniel Nkhilifodi a zaka 29, a Anderson Nkhilifodi azaka 29 ndi a Joseph Sajiwa a zaka 39 powaganizira kuti adapha a Peter David a zaka 22 pankhaniso yolimbirana malo.

M’boma la Mchinji, mudzi wonse wa Chikatipwa kwa T/A Mlonyeni anthu onse adathawapo atavulazana, kugumulirana nyumba, kupherana ziweto ndi kutenthelana nkhokwe patabuka mkangano wa malo.

Izi ndi zina mwa nkhani zomwe zikuchitika m’maboma onse m’dziko muno zomwe zidapangitsa kuti boma liyambitse pulogalamu yoti anthu azilembetsa malo a banja kuti azikhala ndi umboni wa umwini.

Mkulu woyang’anira ntchito younika malamulo okhudza malo ku unduna wazamalo a Masida Mbano adati pulogalamu yoti anthu azilembetsa malo abanja idakhazikitsidwa n’cholinga choteteza anthu ochepekedwa mphamvu.

Anthuwo ndi monga ana amasiye, okalamba, aulumali, akamwini ndi atengwa omwe munthu yemwe amadalira akamwalira amalandidwa malo mosavuta.

“Cholinga choyamba nchoti titeteze anthu opanda mphamvuwa chifukwa anthu adyera amawadyera masuku pa mutu ndiye tikufuna azikhala ndi umboni woti olo ku khothi akhoza kukapeza chilungamo,” adatero a Mbano.

Iwo adati ndi ndondomekoyi, milandu ya malo ikhoza kuchepa chifukwa anthu ena amayamba dala mlandu akudziwa choona koma amatengera danga kuti palibe umboni.

T/A Mwansambo ya ku Nkhotakota yathirira umboni kuti kulembetsa malo a banja n’kothandiza komanso kumapeputsa mafumu ku ntchito yoweruza milandu ya malo.

Iwo ndi mmodzi mwa mafumu omwe adapanga kale pulogalamuyo m’madera mwawo ndipo adati m’miyezi 8 pulogalamuyo isadabwere adaweluza milandu 66 yokhudza malo koma pano milanduyo idatha.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button