Nkhani

Aphungu akana makondomu aulere

Aphungu a Nyumba ya Malamulo Lachitatu adabweza mphatso ya makondomu 206 000 yomwe bungwe la Aids Health Foundation (AHF) lidapereka kunyumbayo.

Aphunguwo adakhumudwa ndi zomwe adanena wapampando wa komiti ya zaumoyo Maggie Chinsinga kuti aphungu, ogwira ntchito kunyumbayo komanso alendo amagwiritsa ntchito makondomu 10 000 pa mwezi.

Koma Lachitatu, aphungu a mbali zonse ziwiri ya boma ndi yotsutsa adanyangala ndi lipotilo lomwe adati ndi lochotsa ulemu komanso lonyazitsa ndipo adagwirizana zobweza mphatso yamakondomuyo.

Wachiwiri woyamba kwa sipikala wa nyumbayo Madalitso Kazombo sadapereke chigamulo chake pamtsutsowo, aphungu osiyanasiyana adapereka maganizo awo osonyeza kunyansidwa.

Pomaliza pa nkhaniyo, Kazombo adavomerezana ndi aphunguwo kuti mawu omwe adanenedwawo adachepsa ulemu wa aphungu ndipo adati mphato yamakondomuyo ibwezedwe komanso Chinsinga apepese.

Mkulu wa bungwe la AHF Triza Hara adati adapereka mphatso ya makondomuyo pofuna kuteteza aphungu, ogwira ntchito ku nyumbayo komanso alendo.

“Aliyense mwa iwo ayenera akhale ndi mpata umenewu odziteteza ku matenda,” adatero Hara.

Malingana ndi Chinsinga, mmbuyomo, nyumbayo imalandira makondomu kuchokera kuofesi ya zaumoyo m’boma la Lilongwe koma kenako idapanga ubale ndi bungwe la Partners in Hope.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button