Nkhani

Akumba manda m’khonde la nyumba

Athu okwiya aika maliro pakhomo pa mkulu wina ku Chirimba mumzinda wa Blantyre yemwe amamanga nyumba panjira yolunjika kuchipata cha manda.

Malingana ndi ena mwa omwe adaona izi zikuchitika ati si koyamba kuti mkuluyo achite zotere chifukwa mmbuyomu adachitanso zotere.

Dalili kulongosola mbali imene malo ake achita malire ndi manda

“Poyamba adamanga mpanda wotchinga msewu wa kumanda ndipo zinatengera amfumu kulamula kuti agumule mpandawo ncholinga choti anthu azitha kudutsa mosavuta,” adatero mmodzi mwa anthuwo, yemwe adakana kutchulidwa dzina.

Kumbali yake, mkuluyo, Henderson Dalili, adati adadabwa kuona T/A Machinjiri akubwera ndi gulu la anthu omwe amati ndi okhumudwa ndi ganizo lake lomanga nyumba pamalo akepo.

“Malowa ndi anga ndipo ndimamanga nyumbayi podziwa kuti ndi malo anga. Apa ndidaona a Machinjiri akubwera ndi gulu la anthu omwe amandiopseza,” adatero Dalili.

Iye adatinso adaganiza zomanga nyumba pamalopa pozindikila kuti mandawo anali pafupi kudzadza.

“Panopa ndikufuna kukumana ndi a Machinjiri kuti ndiwauze kuti ndasiya kumanga nyumbayi ndipo ndikakambirane nawo za tsogolo la malowa,” adatero iye.

Kumbali yake T/A Machinjiri adati zoti Dalili akumanga nyumba pamanda akuzidziwa ndipo kuti anakambirana nawo kunatsala ndi kuwapatsa chigamulo cha papepala sakusamala pomanga nyumba chifukwa chikhalidwe chathu sichilola anthu a moyo kuyandikana ndi manda,” adatero Machinjiri.

Mfumu ya ndodoyo idakana kuthilapo ndemanga pankhani yokhudzana ndi kuikidwa kwa munthu wakufa pamalo pomwe Dalili akubzala maziko a nyumba.

Ndipo Gulupu Magasa ya m’deralo idati zoti a Machinjiri ndi iwo anapita kukakambilana ndi a Dalili pa zomwe achitazo ndi zoona koma adati sakudziwa zoti anthu ayika maliro pamalo omwe akuyika maziko a nyumba..

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button