Nkhani

Aphungu akwangula zokambirana zawo

Mtsogoleri wa Nyumba ya Malamulo a Richard Chimwendo Banda adatseka mkumano wa aphungu Lachitatu ndi langizo kwa otsutsa boma kuti aonjezere mphamvu zawo kuti boma liziyenda bwino.

A Chimwendo amatseka mkumanowo pomwenso adakambirana za ndondomeko ya zachuma ya 2022 mpaka 2023 yomwe aphunguwo adavomereza kuti boma ligwiritse ntchito ndalama zokwana K2.84 triliyoni atakumana kwa sabata 9.

Nduna ya zachuma a Sosten Gwengwe adapereka ndondomeko ya zachuma

Iwo adati boma limayenda bwino ngati mbali yotsutsa ikuonetsa mphamvu poongolera momwe boma likuyendetsera zitukuko zake koma mmalo mwake, mbali yotsutsa boma ikutaya nthawi n’kumangolimbana.

“Tikufuna muzititsutsa osati muzingokangana. Mwangokhala zaka zitatu zokha kotsutsa koma mwagawikana kale nanga komwe mudzakwanitsile zaka 26 ngati anzanufe mbali yotsutsa idzakhalapo,” adatero a Chimwendo Banda.

Kadaulo pa ndale a Ernest Thindwa adayamikira a Chimwendo palangizo lawolo koma adati boma lisamadikile kutsutsidwa kuti lizipanga zooneka chifukwa lidapanga kale ndondomeko yamomwe lidzayendetsele dziko.

“A Chimwendo Banda akunena zoona, mbali yotsutsa imayenera kukhala ya mphamvu kuti boma lisamachite zopepera. Mutengere chitsanzo cha momwe malemu Bingu Wa Mutharika adayendetsera dziko zaka 5 zoyambirira chifukwa otsutsa nthawi imeneyo samasekerera.

“Komabe boma nalo lisamathawire koti silikutsutsidwa mokwanira chifukwa chitukuko sichidikira kutsutsidwa kokhakokha. Otsutsa amangothandizira kuti pomwe pakupotoka paongoke,” adatero a Thindwa.

Mkulu wa mbali yotsutsa boma a Kondwani Nankhumwa adayamikira aphungu podutsitsa bajeti koma adadzudzula zinthu zambiri zomwe sizikuyenda bwino mdziko muno.

“Amalawi akuzunzika chifukwa cha kukwera kwa mitengo ya zinthu. Mafuta ophikira lita imodzi pano ndi K4 000 pomwe malita 5 ndi K20 000. Buledi anali K500 pano ndi K1 000, sopo wa U-fresh adachoka pa K150 pano ndi K300 pomwe shuga adali K800 pano ndi K1 000,” adatero a Nankhumwa.

Iwo adapitiriza kudzudzula pulogalamu ya zipangizo zaulimi zotsika mtengo (AIP), katangale, kufooka kwa chitetezo, ufulu wa atolankhani, njala m’chaka chikubwerachi ndi kusayendetsa bwino chuma cha boma.

“Chaka ndi chaka timadutsitsa bajeti koma sitiunika bwinobwino kuti bajeti ya chaka chatha idayenda bwanji n’chifukwa chake zoipa zomwezi zimapeza malo,” adatero a Nankhumwa.

Nyumbayo idavomereza bajeti ya K2.84 triliyoni osasintha kalikonse koma mkulu wa bungwe la Human Rights Consultative Committee (HRCC) a Robert Mkwezalamba adati aphunguwo aziunika bajeti mwaukadaulo.

“Sitikudziwa kuti kapena bajetiyo idakonzedwa mwaukatswiri kapena aphunguwo adalibe luntha lozukuta bajeti. Mtsogolo muno tidzakonda kuti aphungu azilimbana nayo kwambiri bajeti osamangodutsitsa ayi,” adatero a Mkwezalamba.

Aphunguwo adavomereza mabilo 20 omwe akudikira kuti mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera asainire, adalandira malipoti okhudza ndende komanso lipoti la pachaka la nthambi yothana ndi katangale ndi lipoti lokhudza kayendetsedwe ka chuma.

Nduna zosiyanasiyana zidapereka malipoti a kumaunduna kwawo, makomiti osiyanasiyana adaperekanso malipoti awo, aphungu adali ndi mpata ofusa mafunso kwa nduna ndipo nyumbayo idavomereza mkulu wa majaji komanso membala wa nthambi yoyendetsa Nyumba ya Malamulo.

Related Articles

Back to top button