Nkhani

Aphungu asintha lamulo

Fumbi lakhazikika lokhudza komwe anthu omwe adzakhale akugwira ntchito za chisankho pa nthawi yovota pa September 16 adzaponyere voti yawo.

Izi zadza potsatira kuunikanso kwa lamulo loponyera voti lomwe Nyumba ya Malamulo idapanga Lachiwiri.

Aphungu adakwangula sabata yatha. I Nation

 Ngakhale padali mazangazime kuti kuunikirako kutheke malingana n’kuti otsutsa boma adali ndi mafunso omwe akuoneka kuti adatuluka m’nyumbayo popanda mayankho, pa mapeto pake zidadziwika kuti omwe adzakhale akugwira ntchito yothandizira kuponya voti adzakhala ndi ufulu komwe adzatumidzidwe kukagwira ntchito.

Malingana ndi nduna ya za malamulo a Titus Mvalo, magulu omwe akukhudzidwa ndi achitetezo, ogwira ntchito ku bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) komanso ma monitala oyimilira zipani ndi makandideti.

Ntchito younikira lamulolo idayamba ndi mabungwe oima paokha pansi pa Civil Society Elections Integrity Forum (CSEIF) omwe adachenjeza kuti anthu oposa 50 akhoza kudzalephera kuponya voti.

Wapampando wa CSEIF a Benedicto Kondowe adati lamulolo limasemphana ndi zomwe lamulolo lalikulu (Constitution) limanena kuti munthu aliyense ali ndi ufulu woponya voti ndi kusankha atsogoleri a kumtima kwake.

“Dziko lino silizindikira lamulo lililonse lomwe likukolana ndi lamulo lalikulu. Lamulo lalikulu limanena kuti munthu aliyense yemwe adafika msinkhu oyenera kuvota ali ndi ufulu wovota,” iwo anatero.

Potsatira kuunikirako, mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera adalamula kuti ngakhale Nyumba ya Malamulo idathetsedwa, aphungu akumane Lachiwiri kuti akaunikile gawolo chisankho chisadafike.

Iwo adalamula izi pogwiritsa ntchito gawo 67 (4) lomwe limapereka mphamvu kwa Pulezidenti kuitanitsa nyumbayo ngakhale itathetsedwa.

Koma kudali sewero ku nyumbayo aphunguwo atayamba zokambirana chifukwa ambali yotsutsa boma amati samaona kufunika kwa n’kumanowo.

“Nkhani yaikulu yake iti poti izi takhala tikuziwona m’mbuyo monsemu. Pa zisankho zonse, achitetezo amakaponya voti yawo tsiku lenilenilo lisadafike, ndiye lero zachita kutani kuti mpaka tizikumana muno,” adatero olankhulira chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) pankhani za malamulo a Bright Msaka.

Mfundoyi idagwirizana ndi ya komiti ya za malamulo ku nyumbayo yomwe idati padalibe chifukwa chomveka choti gawo 74 ya malamulo oyendetsera chisankho iunikidwe poti boma lomweli ndilo lidabweretsa Bill yosintha.

“Komiti itaunika bwino nkhaniyi, yaona kuti palibe kufunika kulikonse koti nyumba ino ikhale pansi ndi kuunikira gawolo,” adatero wapampando wakomitiyo a Albert Mbawala.

Polankhulapo pa nkhaniyo, phungu wa chipani cha DPP ku Blantyre City South East a Sameer Suleman adati akuona kuti kuunikira kwa gawolo ndi njira yomwe chipani cha MCP chikufuna kudzagwiritsa ntchito pobera zisankho.

“Ndili ndi umboni kuti akufuna kuti azidzatuma anthu kunamizira kuti ndi achitetezo kapena mamonitala ndi cholinga choti akaponye voti. Iyi ndi njira yongofuna kubera zisankho basi,” adatero a Suleman.

Koma phungu wa Lilongwe Mpenu a Eisenhower Mkaka adapempha a Sipikala a ku nyumbayo a Catherine Gotani Hara kuti alamule a Suleman kuti abwere ndi umboni wa zomwe adanenazo, koma malingana ndi nthawi, pempholo lidali losatheka.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button