MEC yasefa ma kandideti, 17 adutsa
Pomwe kampeni ili mkati, bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) latulutsa maina a ma kandideti omwe akwaniritsa zofunika pa mpando wa pulezidenti.
Mwa makandideti 20 omwe adapereka kalata zofuna kudzapikisana nawo, 17 ndi omwe akwaniritsa zofunikirazo.

Kuyambira pa chiyambi popereka kalatazo, MEC inkalengeza mobwerezabwereza zoyenera kuti kandideti adzakhale nawo pa baloti ndipo idalengezanso kuti okanidwa sadzabwezeredwa K10 miliyoni yomwe adatengera kalata.
“Chonde tsatirani zoyenera kuchita kuwopa kudzakanidwa chifukwa zikadzangochitika kuti kalata zanu zakanidwa kaamba koperewera zoyenera, MEC siidzabweza ndalama,” ankatero wapampando wa bungweli a Annabel Mtalimanja.
Makandideti atatu omwe maina awo sadavomerezedwe ndi a m’busa Hadwick Kaliya, a Danniel Dube a National Patriotic Party ndi a Prophet David Mbewe a Liberation for Economic Freedom Party.
Pa tsiku lotsiriza kupereka kalata za ofuna upulezidenti, mkulu wa MEC a Andrew Mpesi adalengeza kuti makandideti 22 adapereka 10 miliyoni n’kutenga kalata, koma awiri adatsikira panjira.
Malingana ndi a Mpesi, awiriwo ndi a Cassim Chilumpha a Assembly for Democracy and Development (ADD) ndi a Dalitso Chauluka a People’s Progressive Movement (PPM).
Kalata yomwe a Mtalimanja adasayinira, idati:”Tikudziwitsa Amalawi kuti bungwe la MEC litaunika bwinobwino kalata za onse ofuna mpando wa upulezidenti, lavomera mayina 17 kuti ndiwo adzapikisane nawo pa chisankho cha chaka chino.”
Pa nthawi yopereka kalata zawo, a Dube, a Kaliya ndi a Mbewe adapezeka ndi zopelewera ndipo adapatsidwa mpata woti akazikonze n’kukaperekanso ku MEC.
Maina omwe MEC yavomera ndi a Joyce Banda (People’s Party), a Lazarus Chakwera (Malawi Congress Party), a Dalitso Kabambe (UTM Party), a Peter Mutharika (Democratic Progressive Party), a Atupele Muluzi (United Democratic Front), a Kamuzu Chibambo (People’s Transformation) ndi a Frank Mwenifumbo (National Development Party),
Ena ndi a Michael Usi (Odya Zake Alibe Mlandu), a Jordan Sauti (Patriotic Citizens Party), a Akwame Bandawe (Anyamata, Atsikana, Azimayi) ndi a Kondwani Nankhumwa (People’s Development Party).
Makandideti odzayima paokha ndi a Milward Tobias, a Adil James Chilungo, a Smart Swira, a Cosmas Felix Chipojola, a Pemphero Mvula ndi a Thokozani Manyika Banda.
Koma patsamba lawo lamchezo, a Mbewe adauza owatsatira kuti asadandaule chifukwa ali mkati mokambirana za mgwirizano ndi zipani zina ndipo Lachinayi, mlembi wamkulu wa DPP a Peter Mukhito adatsimikiza kuti DPP yapanga mgwirizano ndi chipani cha a Mbewe.



