Nkhani

Aphunzitsi akhoza kuyambanso sitalaka

Masiku 7 omwe bungwe la aphunzitsi la Teachers Union of Malawi (TUM) lidapereka ku boma kuti liwapatse ndalama zomwe adapangana kuti aimitse sitalaka yawo adatha Lachinayi popanda chilichonse kutanthauza kuti aphunzitsiwo akhoza kuyambanso sitalaka.

Wapampando wa bungwelo Willie Malimba watsimikiza kuti masikuwo adatha Lachinayi koma kaamba ka tchuthi cha Pasaka, kudali kovuta kumema aphunzitsiwo kuyamba sitalaka masiku a tchuthi.

“Pali tchuthi pakatipa ndiye sitingachite kalikonse koma pofika Lachiwiri mumva kuti tikulowera kuti ndi sitalaka yathu,” adatero Malimba.

Chikamatha tchuthi cha Pasaka chomwe timakumbukira masautso ndi kuuka kwa Ambuye Yesu, tsiku loyamba kugwira ntchito ndi Lachiwiri koma malingana ndi ndemanga ya Malimba sizikudziwika ngati aphunzitsi adzapite ku ntchito.

Koma gulu la aphunzitsi omwe akuti atopa ndi momwe TUM ikuyendetsera ntchito zake ati sitalakayo ikachitika, iwo amema aphunzitsi anzawo kuti achite mademo okhaulitsa atsogoleri a TUM.

Gululo lomwe likutchedwa kuti ‘Liwu la aphunzitsi okhudzidwa’ lati likukayikira atsogoleri ena a bungwero kuti akutumikira andale ena omwe cholinga chawo n’kusokoneza maphunziro a m’sukulu za boma pomwe ana awo ali m’sukulu zomwe si zaboma.

Malingana ndi konsititushoni ya TUM, adindo amayenera kukhala pampando kwa zaka zitatu ndipo adindo omwe alipowa motsogozedwa ndi Malimba akwanitsa zakazo chaka chino koma aphunzitsi okhudzidwawo ati asadikire nthawi ya zisankho kuti adindowo achoke.

“Akusokoneza aphunzitsi amenewa, bwanji angoitanitsa zisankho kuti aone ngati aphunzitsi akuwafunanso,” adatero wapampando wa gululo Stafuel Chitukuta.

Gululi lidali loyamba kuuza boma kuti aphunzitsi akufunika ndalama ya ukadziotche pa 20 November 2020 ndipo TUM idawakhira n’kuyamba zokambirana ndi boma koma kaamba kosamvana, nkhaniyi idabutsa sitalaka ya apahunzitsi.

Kenako gululo litaona kuti sitalakayo ikulowera kwina, pa 8 March 2021 lidaitanitsa msonkhano wa atolankhani komwe idakafotokoza kuti aphunzitsiwo atopa ndi sitalaka ndipo sakufunaso ndalama ya ukadziotcheyo.

Kadaulo pa zamaphunziro Benedicto Kondowe adadzudzula kale kuti Pulezidenti Lazarus Chakwera akuyenera kulowererapo pa sitalakayo chifukwa ikupita kolakwika.

Chitukuta adati aphunzitsi akudabwa kuti TUM ikukoka nkhani ya ndalama za ukadziotche pomwe aphunzitsi adakatula nkhani zambirimbiri zokhudza kutukula miyoyo yawo zomwe mpaka pano TUM siyidaperekepo ndemanga yake.

Related Articles

Back to top button