Nkhani

Athana naye Chizuma

Listen to this article

Mkulu wa bungwe lolimbana ndi katangale ndi ziphuphu a Martha Chizuma akadali ndi ulendo wautali woteteza ntchito yawo yothana ndi anthu omwe akukhudzidwa ndi nkhani zakatangale komanso ziphuphu m’dziko muno.

Lachitatu lapitali, a Chizuma adalandira kalata kuchokera ku ofesi ya Pulezidenti ndi nduna yosainidwa ndi mlembi wa ofesiyo a Colleen Zamba yowaimitsa ntchito mpaka milandu yomwe akuyankha ithe.

A Zamba ndi a Chizuma pa msonkhano wokambirana zakatangale

Izi zikuchitika pomwe m’manja mwa a Chizuma muli mafailo ochuluka okhudza zakatangale ndipo iwo adanenapo m’mbuyomo kuti pa mndandanda womwe alinawo, palinso maina ena a nduna ndi akuluakulu m’boma.

Pa tsiku lokumbukira kuthana ndi katangale ndi ziphuphu chaka chatha, a Chizuma adagwedeza dziko atanenetsa pamaso pa mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ndi nduna zaboma kuti sakuopa kanthu ndipo athana ndi aliyense amene ali m’mafailo awo.

“Ntchito yanga n’kuthana ndi katangale ndi ziphuphu ndiye sindiopa kuti munthu ndiotchuka bwanji, ali ndi ndalama zochuluka bwanji kapena kuti ndi wandale. Ngati mphepo yandipeza kuti adapangapo katangale, akwekwesedwa,” iwo adatero.

Owaimilira pa milandu a Martha Kaukonde adatsimikiza zoti a Chizuma adalandira kalata yowaimitsa ntchito. Koma adati n’zodabwitsa chifukwa adawaimitsa ntchito chifukwa cha mlandu womwe sadapelekere umboni.

“N’zoona awaimitsa, koma n’zodabwitsa chifukwa mlandu omwe akunenawo sitidakalowe [m’khoti] tidzalowa pa 8 February 2023,” adatero a Kaukonde.

Polankhulapo, wapampando wa komiti yoona zamalamulo ku Nyumba ya Malamulo a Peter Dimba adati kuimitsidwa kwa a Chizuma ndinkhani yomvetsa chisoni ndipo yoonekeratu kuti atcheredwa.

“Ndife odabwa komanso okhudzidwa kuti akuluakulu athu akuyesetsa kufuna kukankhira dzikoli kuphedi. Zikutidabwitsa kwambiri komabe izizi zidawonekera patali pomwe,” adatero a Dimba.

Ndipo mkulu wa bungwe la Centre For Democracy and Economic Development Initiative (Cdedi) a Silvestre Namiwa ati akuona kuti chachuluka pankhaniyi n’kufuna kutetezana pakati pa akuluakulu omwe akudziwana kuti adapanga zakatangale.

A Namiwa ati pazomwe zachitikazo, boma la a Chakwera liyenera kubwera poyera kuwuza Amalawi ngati sakufuna bungwe lolimbana ndi katangale pa ulamuliro wawo m’malo mongophimba Amalawi m’maso.

“N’chifukwa chiyani nkhani iyiyi imangobwerabwera? Kapena akungofuna kutetezana?. Angotiuza ngati sakufuna bungwe la ACB pa ulamuliro wawo,” adatero a Namiwa.

Kadaulo wa zamalamulo a Garton Kamchedzera adauza The Nation kuti a Chakwera akudzikolakola okha chifukwa adalonjeza pagulu kuti a Chizuma akhalabe mkulu wa ACB.

Related Articles

Back to top button