Nkhani

Awachotsa pa mpando atayendera a Bushiri

Kadaulo pa ndale kuno ku Malawi a George Chaima komanso wa ku South Africa a Dr Zwakala ati payenera kukhala nkhani yaikulu pa kuchotsedwa kwa a Floyd Shivambu ngati mlembi wamkulu wa chipani cha uMkhonto weSizwe (MK).

 Chipanicho chidachotsa a Shivambu pa mpandowo pa chifukwa choti iwo adadzayendera a Prophet Shepherd Bushiri m’mwezi wa April 2025 ponena kuti adaphwanya malamulo a chipani omwe amanena zomwe atsogoleri angapange komanso ayi.

Adakumana nthawi ya Pasaka: A Bushiri ndi a Shivambu. | Nation

 M’chikalata chomwe chipanicho chidatulutsa ndipo chidasainidwa ndi mtsogoleri wake a Jacob Zuma, chipanicho chidati a Shivambu adaphwanya gawo 3 (j) la malamulo ake.

 “Zomwe adapanga a Shivambu n’zosemphana ndi malamulo a chipani chathu. Potengera kukula kwa mlanduwu komanso posamala mbiri ya chipani, a pulezidenti ndi akuluakulu ena ku chipani sakadachitira mwina koma kupanga chiganizochi,” chidatero chikalatacho.

 Akadaulo ena komanso nzika ndi mabungwe m’dziko la South Africa akuti akuona ngati mchitidwe wa a Shivambu udachepsa mphamvu za nthambi ya za malamulo m’dzikolo chifukwa limatenga a Bushiri ngati mdani wake yemwe adaphwanya malamulo ake.

 Koma polankhula ndi Tamvani, a Chaima adati kulikonse, malamulo amalola munthu aliyense kuyenda ndi kuyendera aliyense m’dziko lililonse pokhapokha ngati pali chiletso chapadera pa munthuyo zomwe palibe pa a Shivambu.

“Tikatsatira nkhani yonse, a Shivambu adabwera ngati iwowo osati kuimira dziko kapena chipani ndiye nzosamveka kuti kubwera kwawo kukutanthauza kuderera nthambi ya za malamulo m’dzikolo ayi si zoona. Chilipo chifukwa chomwe sakuchinena,” adatero a Chaima.

 Iwo adati a Bushiri adachita zomwe munthu aliyense angachite moyo wake utakhala pachiwopsezo ndipo adatsindika kuti dziko la Malawi ndi South Africa ali pa ubale wabwino omwe sufunika ndale kulowererapo kuopa kusokoneza.

A Zwakala adauza Newsroom Africa kuti: “Pali nkhani ina pa kuchotsedwa kwa a Shivambu ngati mlembi wamkulu wa chipani cha MK kuposa kuyendera a Bushiri.”

 Chipani cha MK chitachotsa a Shivambu pa mpando wa mlembi wamkulu, chidawapatsa udindo wina wochiimirira ku Nyumba ya Malamulo koma anthu ena m’dzikolo akupereka maganizo oti izinso zikhoza kuononga mbiri ya chipani cha MK.

Kadaulo wa kayendetsedwe ka zinthu ku South Africa a Mazwe Majola adalosera kuti a Shivambu adzalandira chilango ku chipani kwawo kaamba koyendera a Bushiri ulendo wawo utangochitika kumene.

 Iwo adauza BBC kuti: “Ndikukhulupilijra kuti chipani cha MK chipangapo kanthu, ngakhale kuti a Shivambu adayendera zawo, koma mbiri ya chipani ikukhudzidwa apapa ndipo ndili ndi chikhulupiriro chonse kuti awapatsa chilango.”

 A Bushiri ndi banja lawo adathawa m’dziko la South Africa m’chaka cha 2020 ali pa belo pa milandu ingapo kuphatikizapo wozembetsa ndalama za dzikolo koma dziko la South Africa lakhala likukakamiza dziko la Malawi kuti litumize a Bushiri m’dzikolo kuti akayankhe milanduyo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button