Nkhani

‘Boma latipaka mafuta pakamwa’

Listen to this article

Ogwira ntchito m’boma ena ati boma lawapaka mafuta pakamwa powalonjeza kuti malipiro awo akwera ndi K61 pa K100 iliyonse kuyambira mwezi wa March chifukwa malipirowo sanakwere monga boma lidalonjezera.

Iwo auza Tamvani m’sabatayi kuti ena malipiro awo akwera pomwe ena sadakwere. Iwo atinso ngakhale magiledi afanana koma kakwezedwe kakusiyana pomwe ena adakaphulabe njerwa zamoto.

Boma ndi anthu ogwira ntchito m’bomawa adagwirizana za malipirowa m’mwezi wa February chaka chino pomwe antchitowa adachita zionetsero sabata ziwiri pokakamiza boma kuti lisunthe malipiro awo.

Iwo amati bomali likweze ndi K67 pa K100 iliyonse koma boma lidati likwanitsa kukweza ndi K61. Mgwirizanowo udati omwe amalandira ndalama zochepetsetsa ndiwo alandire K61 ndipo nambalayo izichepa mpaka kufika pa K5 kwa bwana kwambiri m’boma.

Mphunzitsi wina yemwe ali m’giledi L-4 kusukulu ina m’boma la Ntcheu wati kumeneko aphunzitsi adakhalirana pansi kuti aone momwe alandirira malipiro.

“Amene talandira bwino ndi ife a giledi L-4. Giledi imeneyi ndiyo yotsikitsitsa kwa aphunzitsi. Malipiro athu akwera ndi K2 000 pomwe ena asintha ndi K500 ena sadawawonjezere kalikonse.

“Omwe talandira bwinofe ndi amene tikulimba ndi ntchito chifukwa tikutengedwa kuti tikulandira bwino kusiyana ndi anzathu. Maphunziro asokonekera kale, nthawi zonse tikungokambirana zimenezi kusiya kuphunzitsa,” adatero mphunzitsiyo yemwe ankalandira K29 000.

Ogwira ntchito kuchipatala akuti malipiro a ena akwera pomwe ena adakali pakale.

“Mu giledi yathu timalandira K26 000 koma pano ena zawayendera pomwe alandira K34 000 koma ine palibe chasintha. Tikusowa kuti tifunsa ndani,” adatero wina.

Malinga ndi wapolisi wina, wapolisi yemwe amalandira ndalama zotsikitsitsa ndi constable yomwe ndi K32 000. Malinga ndi kusintha kwa malipiro ma constable ena awakwezera ndi K1 000.

“Zikuvuta kuzimvetsa, palibe akwezapo apa chifukwa momwe zinthu zakwerelamu sangakweze malipiro ndi K1000. Moyo wamavuto ukupitiriza ndipo izi sizichepetsabe mchitidwe wa ziphuphu pakati pa apolisi,” adatero wapolisiyo akuvomerezana ndi wapolisi wina yemwe amati malipiro ake sadasinthe.

Koma kwa mamesenjala zinthu akuti zili bwino pomwe aona ulemerero ndi kukwera mtengo kwa malipiro awo. Ena omwe tidacheza nawo ku depatimenti yoona zolowa ndi kutuluka ya Immigration adati malipiro akwera kuchoka pa K19 000 akadulidwa msonkho kufika pa K31 000.

“Ayi bolani kusiyana ndi poyamba,” adatero mesenjala wina akugula mandasi kumeneko.

Koma mkulu wa bungwe loona ufulu wa anthu ogwira ntchito m’boma la Civil Servants Trade Union (MCTU), Elijah Kamphinda Banda sadakane kapena kuvomereza za nkhaniyi ponena kuti mgwirizano omwe anthuwa ndi boma adapanga ukuwonedwabe.

“Bvutoli litha kukhala loona poti makonzedwe ake anali othamanga kwambiri poganizira za ntchito zomwe zidaima [pomwe timakakamiza boma kuti likweze malipiro]. Komabe pokambirana mbali zonse zidagwirizana kuti wolandira K18 000 adutse pa K29 000 ndipo izi zidachikadi.

“Panopa zokambirana zili mkati malingana ndi mgwirizano wa mbali ziwirizi kuti pofunuka kuthetsa zolakwika za malipirowa kuti mu July adzakhale atsopano,” adatero Kamphinda.

Iye adafotokozapo momwe kuwonjezerako kudachitikira. “Mwachitsanzo wolandira zochepa adaonjezeredwa ndi K11 000 kutanthauza kuti mwa ndalama zimenezi K3 300 yapita ku msonkho ndipo munthuyu watsala ndi K7 700 basi. Ndi chifukwa timanena kuti ndife akapolo a msonkho.”

Iye adatinso bungwe lawo lidzanena chomwe lingachite ngati zokambiranazi sizingathe bwino potsindika kuti pofika July zonse zikhala zitayera.

Mneneri wa boma, Moses Kunkuyu wati oimira anthu ogwira m’bomawa omwe amakambirana ndi boma amayenera kufotokozera anthu awo za momwe malipirowo akhalire asadayambe kusangalala kuti malipiro akwera.

“Omwe amayenera kulandira K61 ndi omwe akulandira ndalama zochepetsetsa. Malipirowo amanka nasintha malinga ndi giledi yomwe munthu ali. Ngati anthu aona kuti malipiro asintha asadabwe ndizo tidagwirizana,” adatero Kunkuyu.

Koma pankhani yoti ena akulandira malipiro osiyana koma giledi imodzi iye adati: “Imeneyo ndiye yoyenera kukhalira pansi ndikuona kuti pavuta ndi pati. Anthu omwe amaimira anthuwa bwezi atabwera ndi nkhaniyi ndikupeza pomwe padakhota kuti zotere zichitike.”

Related Articles

Back to top button