Chilimikani pa ulimi—Kazembe

Malinga ndi ng’amba imene yasautsa m’madera ambiri m’dziko lino, wachiwiri kwa kazembe wa limodzi mwa maiko a ku Ulaya la Flanders, Nikolas Bosscher wati boma la Malawi liyenera kuika mtima potukula ulimi m’dziko muno.

Bosscher adanena izi Lolemba pa msonkhano wa dzidzidzi wa komiti ya National Agricultural Content Development Committee (NACDC).

Iye adati kuti dziko lino lithane ndi mavuto akudza chifukwa cha kusintha kwanyengo, n’kofunika kubweretsa chitukuko chachikulu kumbali ya ulimi.

“Dziko la Malawi silikuchita chitukuko chenicheni kumbali ya ulimi chifukwa ndalama zambiri zikumapita kundondomeko yopereka zipangizo zaulimi motsika mtengo ndi kugula chimanga zomwe sizingamange maziko olimba otukula ulimi,” adatero iye.

Iye adati ulimi ukumakhudzidwa ndi china chilichonse chokudza monga ng’amba, tizilombo toononga mbewu, matenda ngakhale kusowa kwa misika kumene. Choncho boma liyenera kuika patsogolo ndikubweretsa chitukuko kumbali ya ulimi.

“Monga madera omwe chimanga chaumiratu, mlimi ayenera kuuzidwa kuti azule chimangacho ndikubzala mbewu zina monga chinangwa ndi mbatata,” adalongosola Bosscher.

Mkulu wa nthambi ya ulangizi ku unduna wa zaulimi Jerome Nkhoma yemwe adali nawo pa msonkhanowo adati boma laika kale mtima pa chitukuko ndipo mwazina lidaika mlozo womwe kampani zingatsate pobweretsa chitukuko kumbali ya ulimi.

Nkhoma adati nkofunika kuti alimi apatsidwe uthenga oyenera mwachangu okhudzana ndi ulimi pothana ndi vutoli.

Ndipo Farm Radio Trust, bungwe lomwe limathandiza kufalitsa uthenga kwa alimi, yomwe idaitanitsa msonkhanowo idati zinthu sizili bwino m’dziko muno ndipo alimi ambiri akhudzidwa ndi ng’amba ndi mbozi zomwe zikuononga mmera.

“Ngakhale tidauzidwa kuti kukhala ng’amba komanso mbozi zoononga mmera, sitimayembekezera kuti vutoli likhala lalikulu chonchi,” adatero George Vilili wochokera ku bungwelo.

Pomwe mkulu wa nthambi yoona zanyengo Jolamu Nkhokwe adati nthambi yake idanena kuti chaka chino kukhala ng’amba komanso madzi osefukira mwezi wa September chaka chatha.

Nkhokwe adati mvula ikadali kugwa, ndipo Madera ena omwe mudagwa ng’amba, alandira mvulayi komabe adalimbikitsa alimi kutsatira uthenga omwe nthambi yake imapereka nthawi ndi nthawi.

Share This Post