Nkhani

MEC ikufunakusinthatsiku la chisankho

Listen to this article

Pavuta kuti chisankho chichoke mwezi wa May kupita September monga bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidapemphera komitiya Nyumbaya Malamulo yoona zamalamulo.

Mkulu wa MEC, Jane Ansah sabata yatha adapempha komitiyo kuti ilingalire za ganizoli.

Iye adati izi zikudza chifukwa mwezi wa May ndiwozizira komanso usiku umatalika kuposa tsiku, zimene zingachititse ena kulephera kuvota. Malinga ndi malamulo, chisankho chiyenera kuchitika sabata yachitatu mwezi wa May ndipo ngati kusinthako kungachitike pachisankho cha 2019, ndiye kuti mtsogoleri wadziko lino Peter Mutharika akhala pampandowo miyezi 4 yoonjezera.

Koma mneneri wachipani chotsutsa cha Malawi Congress Party (MCP) Ezekiel Ching’oma komanso mkulu wabungwe losanthula zandale la Institute for Policy Interaction (IPI), Rafiq Hajat ati izon’zosatheka.

Ching’oma Lachinayi adati a Malawi atopa ndiboma la DPP ndipo sadakonzeke kuti mpaka akhalebe ndinthawi yaitali asadachotse chipanicho m’boma.

“Ndizachilendo kumva kuti masiku akufuna asinthidwe. Mwezi wa May sidziko lonse limakhala ndi nyengo yozizira. Akufuna achitenji? Ife a MCP takana zimenezo,” adatero iye.

Hajat adamema zipani ndi mabungwe kuti akane ganizo la MEC ponena kuti ntchito yosintha tsiku siyophweka.

“Popanga tsiku padali nthawi komanso mbali zonse zofunikira zimene zidapezeka kuti apange lamulo. Kutanthauza kuti pali ndime kuti tsikuli lisinthe. Komanso sindikuona kufunika kwake. Amabungwe ndi zipani akane,” adatero Hajati.

Koma kadaulo pa malamulo Edge Kanyongolo akuti ganizo la MEC losintha tsikuli ndilochitika.

“Ndizotheka palibe chovuta,” adatero Kanyongolo.

“Chofunika nkhaniyo ipite ku Nyumba ya Malamulo kuti ikakambidwe ndi aphungu. Apo ayi, phungu wina athakukaiyambitsa kumeneko kuti aikambirane.”

Iye adati aka sikoyamba nkhaniyi kuchitika. “Ngati sindikulakwitsa mu 1999 zotere zidachitika. Nachonso chipani cha Republican Party [RP] chidatengera MEC kubwalo lamilandu pankhani ngati yomweyi. Palibe chachilendo ndiponso palibe chosatheka. Ndizotheka ngati atafuna,” adaonjeza Kanyongolo.

Iye adati maiko ena amangotchu latsiku la chisankho osati mpaka kukhala ndi tsiku lenileni lochititsa chisankho. “Kodi patsiku lachisankho kutachitika chivomerezi mungapite kukavota? N’chifukwa anzathu sakhala ndi tsiku lenileni,” adatero iye.

Mneneri wa chipani cha UDF Ken Ndanga adati sadalondoloze bwino zokambirana zomwe zimachitika pakati pa MEC ndi azipani kotero sangaike mlomo.

Komabe Ndanga adati tilankhule ndi mlembi wa chipanichi Kandi Padambo amene foni yake samayankha.

Nakonso ku DPP sikudachokere mawu pamene Francis Kasaila yemwe ndi wolankhulira chipanichi samayankha foni yake.

Malinga ndi mkulu wamgwirizano wa mabungwe okhudzidwa ndikuyendetsa zachisankho la Malawi Electoral Support Netwrok (Mesn) Steve Duwa adati ganizo losinthalo lidadza atakambirana ndi MEC.

Related Articles

Back to top button
Translate »